5Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa mwa anthu amaikidwa kuti achite utumiki wa Mulungu m’malo mwa anthu,+ kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.+
26 Pakuti mkulu wa ansembe ngati ameneyu ndiyedi wotiyenerera.+ Iye ndi wokhulupirika,+ wosalakwa,+ wosaipitsidwa,+ wosiyana ndi anthu ochimwa,+ ndipo wakwera pamwamba kwambiri kuposa kumwamba.+