Salimo 37:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.+Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.+ Yesaya 13:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 “Taonani! Tsiku la Yehova likubwera. Tsikulo n’lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto. Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chodabwitsa,+ ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa a m’dzikolo.+ Zefaniya 1:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi,+ chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+
10 Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.+Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.+
9 “Taonani! Tsiku la Yehova likubwera. Tsikulo n’lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto. Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chodabwitsa,+ ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa a m’dzikolo.+
18 Siliva kapena golide wawo sadzawapulumutsa pa tsiku la mkwiyo wa Yehova.+ Moto wa mkwiyo wake udzanyeketsa dziko lonse lapansi,+ chifukwa iye adzafafaniza anthu onse okhala padziko lapansi.”+