3 Atakhala pansi m’phiri la Maolivi, ophunzira anafika kwa iye mwamseri ndi kunena kuti: “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo* kwanu+ ndi cha mapeto a nthawi* ino chidzakhala chiyani?”+
13 Achite zimenezi mpaka atalimbitsa mitima yanu ndi kukupangitsani kukhala opanda cholakwa+ ndi oyera pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate, pa nthawi ya kukhalapo*+ kwa Ambuye wathu Yesu, limodzi ndi oyera ake onse.+