9 Koma ena anapitiriza kuumitsa mitima yawo osakhulupirira,+ ndipo anali kunena zonyoza Njirayo+ pamaso pa khamu la anthu. Choncho iye anawachokera+ n’kuchotsanso ophunzirawo pakati pawo.+ Ndipo tsiku ndi tsiku anali kukamba nkhani m’holo pasukulu ya Turano.