6 Ndinaona mngelo winanso akuuluka chapafupi m’mlengalenga.+ Iye anali ndi uthenga wabwino+ wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse.+