-
Ekisodo 25:17-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Mudzapange chivundikiro chagolide woyenga bwino, masentimita 110 mulitali ndi masentimita 70 mulifupi.+ 18 Mupangenso akerubi awiri agolide. Akhale osula ndipo muwaike kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+ 19 Kerubi mmodzi akhale kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina akhale kumbali inayo. 20 Akerubiwo atambasule mapiko awo nʼkuwakweza mʼmwamba ndipo aphimbe chivundikirocho ndi mapiko awo.+ Iwo akhale moyangʼanizana, koma nkhope zawo ziweramire pachivundikiro.
-