-
Ekisodo 37:6-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Anapanga chivundikiro chagolide woyenga bwino+ masentimita 110 mulitali ndi masentimita 70 mulifupi.+ 7 Anapanganso akerubi awiri+ agolide. Anali osula ndipo anawaika kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+ 8 Kerubi mmodzi anamuika kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina anamuika kumbali inayo. Akerubiwo anawapanga kumapeto onse awiri a chivundikirocho. 9 Mapiko a akerubi awiriwo anawakweza mʼmwamba nʼkuwatambasula ndipo anaphimba chivundikirocho ndi mapiko awo.+ Akerubiwo anakhala moyangʼanizana ndipo nkhope zawo zinaweramira pachivundikirocho.+
-