Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 21:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Choncho iwo anayamba kudandaula motsutsana ndi Mulungu komanso Mose+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani munatitulutsa mʼdziko la Iguputo kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya komanso madzi,+ ndipo chakudya chonyansachi chafika potikola.”+

  • Deuteronomo 8:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 musakalole kuti mtima wanu ukayambe kunyada+ nʼkukuchititsani kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo,+

  • Deuteronomo 8:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 anakudyetsani mana+ mʼchipululu, chakudya chimene makolo anu sankachidziwa, kuti akuphunzitseni kudzichepetsa+ komanso kukuyesani kuti mʼtsogolo zinthu zidzakuyendereni bwino.+

  • Yoswa 5:11, 12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Tsiku lotsatira, iwo anayamba kudya zokolola za mʼdzikomo. Pa tsikuli anayamba kudya mikate yopanda zofufumitsa+ ndiponso tirigu wokazinga. 12 Mana analeka kugwa pa tsikuli, pamene Aisiraeli anadya zokolola za mʼdzikomo. Kuyambira pamenepo, sipankakhalanso mana oti Aisiraeli azidya.+ Choncho chaka chimenechi nʼchimene iwo anayamba kudya zokolola za mʼdziko la Kanani.+

  • Yohane 6:31, 32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Makolo athu anadya mana mʼchipululu,+ monga mmene Malemba amanenera kuti: ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+ 32 Kenako Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni chakudya chochokera kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba.

  • Yohane 6:58
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 58 Chimenechi ndi chakudya chimene chinachokera kumwamba. Nʼchosiyana ndi chakudya chimene makolo anu anadya koma nʼkumwalirabe. Aliyense wakudya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha.”+

  • 1 Akorinto 10:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti makolo athu akale, onse anali pansi pa mtambo+ ndipo onse anawoloka nyanja.+

  • 1 Akorinto 10:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Onse ankadya chakudya chauzimu chofanana.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena