Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 39:7-9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kenako, mkazi wa mbuye wake anayamba kuyangʼana Yosefe momusirira, moti ankamuuza kuti: “Ugone nane.” 8 Koma Yosefe ankakana ndipo ankauza mkazi wa mbuye wakeyo kuti: “Mbuye wanga sadera nkhawa chilichonse mʼnyumba muno chifukwa cha ine, ndipo chilichonse chimene iye ali nacho wachisiya mʼmanja mwanga. 9 Mʼnyumba muno mulibe woyangʼanira woposa ine, ndipo mbuye wanga anaika chilichonse mʼmanja mwanga kupatulapo inuyo, chifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingachitirenji choipa chachikulu chonchi nʼkuchimwira Mulungu?”+

  • Deuteronomo 5:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Musachite chigololo.+

  • Miyambo 6:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Aliyense wochita chigololo ndi mkazi ndi wopanda nzeru.*

      Amene amachita zimenezi amadzibweretsera mavuto aakulu pa moyo wake.+

  • Mateyu 5:27, 28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 Inu munamva kuti anati: ‘Musachite chigololo.’+ 28 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyangʼanitsitsa mkazi+ mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.+

  • Aroma 13:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Chifukwa malamulo onena kuti, “usachite chigololo,+ usaphe munthu,+ usabe,+ usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili mʼmawu awa akuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+

  • 1 Akorinto 6:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Thawani chiwerewere.*+ Tchimo lililonse limene munthu angachite ndi la kunja kwa thupi lake, koma amene amachita chiwerewere amachimwira thupi lake.+

  • Aheberi 13:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posadetsedwa,+ chifukwa Mulungu adzaweruza achiwerewere* ndiponso achigololo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena