-
Ekisodo 29:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Kenako utenge chidale cha nkhosa yoikira+ Aroni kuti akhale wansembe ndipo uchiyendetse uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyo idzakhale yako. 27 Pankhosa yoikira Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, upatule chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, ndi mwendo wa gawo lopatulika umene anapereka.+
-
-
Levitiko 7:34, 35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Ine ndikutenga chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku ndiponso mwendo womwe ndi gawo lopatulika. Ndikutenga zimenezi pansembe zamgwirizano za Aisiraeli nʼkuzipereka kwa Aroni wansembe ndi ana ake. Limeneli ndi lamulo kwa Aisiraeli mpaka kalekale.+
35 Limeneli linali gawo la Aroni ndi ana ake monga ansembe. Gawoli linali lochokera pansembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, malinga ndi zimene anawalamula pa tsiku limene anaperekedwa kuti atumikire monga ansembe a Yehova.+
-