-
Aheberi 5:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa pakati pa anthu, amaikidwa kuti azigwira ntchito ya Mulungu mʼmalo mwa anthu,+ kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.+ 2 Amakhala woleza mtima pochita zinthu ndi anthu osadziwa kanthu komanso olakwa,* chifukwa iyenso ali ndi zofooka. 3 Ndipo chifukwa cha zimenezo, amafunika kupereka nsembe za machimo ake, ngati mmenenso amaperekera nsembe za machimo a anthu ena.+
-