-
2 Mbiri 8:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Anatsatira dongosolo la tsiku ndi tsiku loperekera nsembe mogwirizana ndi lamulo la Mose. Nsembezo zinali za pa Masabata,+ za pa masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi za pa zikondwerero zomwe zinkachitika katatu pa chaka.+ Zikondwererozo zinali Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ Chikondwerero cha Masabata+ ndi Chikondwerero cha Misasa.+
-
-
Nehemiya 10:32, 33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Kuwonjezera pamenepo, tinalonjeza kuti chaka chilichonse aliyense azipereka ndalama zasiliva zolemera magalamu 4* kuti akazigwiritse ntchito pa utumiki wapanyumba* ya Mulungu wathu.+ 33 Akazigwiritsenso ntchito pokonza mkate wosanjikiza,*+ nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse, nsembe yopsereza yoperekedwa nthawi zonse pa Masabata+ ndi pa masiku amene mwezi watsopano waoneka,+ madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika, nsembe yamachimo+ yophimba machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse zapanyumba ya Mulungu wathu.
-