-
Numeri 18:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Chamoyo chilichonse choyamba kubadwa+ chimene azipereka kwa Yehova, kaya ndi munthu kapena nyama, chizikhala chako. Komabe uzionetsetsa kuti wawombola mwana woyamba kubadwa wa munthu+ komanso mwana woyamba kubadwa wa nyama yodetsedwa.+ 16 Mwanayo akakwanitsa mwezi umodzi kapena kuposerapo uzimuwombola ndi mtengo wowombolera. Uzimuwombola pa mtengo umene anaikiratu wa masekeli asiliva 5,*+ mogwirizana ndi sekeli lakumalo oyera* lomwe ndi lokwana magera 20.*
-