23 Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mchemwali wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anamʼberekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+
33 Izi ndi zimene mabanja a ana a Merari+ azichita monga mbali ya utumiki wawo pachihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni,+ ndi amene aziyangʼanira utumiki wawo.”
8 Ana a Merari anawapatsa ngolo 4 ndi ngʼombe zamphongo 8, mogwirizana ndi zimene zinkafunika pa ntchito yawo imene ankagwira moyangʼaniridwa ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.+