-
Numeri 3:36, 37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
36 Ntchito imene ana a Merari anapatsidwa inali yosamalira mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake, zitsulo zokhazikapo mafelemu ndi zipilala, ziwiya zake zonse+ ndi ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+ 37 Ankasamaliranso zipilala za mpanda wozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo+ komanso zikhomo ndi zingwe zake.
-
-
Numeri 4:31-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Zinthu zimene azinyamula,+ mogwirizana ndi utumiki wawo pachihema chokumanako ndi izi: Mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake ndiponso zitsulo zokhazikapo zipilala ndi mafelemu.+ 32 Azinyamulanso zipilala+ zozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo,+ zikhomo+ ndi zingwe zolimbitsira mpandawo limodzi ndi zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumiki umenewu. Munthu aliyense muzimupatsa katundu woti azinyamula. 33 Izi ndi zimene mabanja a ana a Merari+ azichita monga mbali ya utumiki wawo pachihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni,+ ndi amene aziyangʼanira utumiki wawo.”
-