Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 12:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Muzidya mkate wopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ Pa tsiku loyamba muzichotsa mʼnyumba zanu ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa chifukwa aliyense wodya mkate wokhala ndi zofufumitsa, kuchokera pa tsiku loyamba kukafika pa tsiku la 7, munthu wochita zimenezi aziphedwa kuti asakhalenso mu Isiraeli.

  • Levitiko 23:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pa tsiku la 15 la mwezi umenewu, muzichitira Yehova Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+

  • Deuteronomo 16:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Musamadye nsembeyo limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Kwa masiku 7 muzidya mkate wopanda zofufumitsa, umene ndi mkate wamasautso, chifukwa munatuluka mofulumira mʼdziko la Iguputo.+ Muzichita zimenezi kuti muzikumbukira tsiku limene munatuluka mʼdziko la Iguputo, masiku onse a moyo wanu.+

  • 2 Mbiri 30:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Hezekiya anatumiza uthenga kwa Aisiraeli+ ndi Ayuda onse ndipo analembera makalata anthu a ku Efuraimu ndi ku Manase+ kuti abwere kunyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzachitira Pasika Yehova Mulungu wa Isiraeli.+

  • 2 Mbiri 30:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Choncho Aisiraeli amene anali ku Yerusalemu anachita Chikondwerero cha Mkate Wopanda Zofufumitsa+ mosangalala kwambiri kwa masiku 7.+ Alevi ndi ansembe ankatamanda Yehova tsiku ndi tsiku nʼkumaimbira Yehova mokweza ndi zipangizo zawo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena