-
1 Mbiri 16:41, 42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
41 Iwowa anali limodzi ndi Hemani ndi Yedutuni+ ndiponso amuna onse amene anawasankha mochita kuwatchula mayina kuti azithokoza Yehova,+ chifukwa “chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”+ 42 Hemani+ ndi Yedutuni anawasiya kuti aziimba malipenga, zinganga ndi zipangizo zina zimene ankagwiritsa ntchito potamanda Mulungu woona* ndipo ana a Yedutuni+ anali alonda apageti.
-