-
Esitere 9:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Izi zinali choncho chifukwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ amene ankadana ndi Ayuda onse, anawakonzera Ayudawo chiwembu kuti awaphe.+ Ndiponso iye anachita Puri+ kapena kuti maere, nʼcholinga choti awasokoneze maganizo nʼkuwapha. 25 Koma Esitere atakaonekera kwa mfumu, mfumuyo inalemba+ lamulo lakuti: “Chiwembu chimene anakonzera Ayuda+ chimubwerere iyeyo.” Choncho Hamani komanso ana ake anawapachika pamtengo.+
-