-
Yesaya 49:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Yehova wanena kuti:
“Pa nthawi yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha.+
Ndipo pa tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza.+
Ndinkakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,+
Kuti ndikonzenso dzikolo,
Kuti anthuwo atengenso cholowa chawo chimene chinali bwinja,+
Ndiponso amene ali mumdima+ kuti, ‘Bwerani poyera kuti anthu akuoneni!’
Iwo adzadya msipu mʼmphepete mwa msewu,
Ndipo mʼmphepete mwa njira zonse zimene zimadutsidwadutsidwa* mudzakhala malo awo odyeramo msipu.
-
-
Yesaya 61:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
61 Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+
Chifukwa Yehova anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+
Anandituma kuti ndikamange mabala a anthu osweka mtima,
Kuti ndilengeze za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,
Komanso kuti maso a akaidi adzatsegulidwa.+
-