-
Machitidwe 10:37, 38Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Inu mukudziwa nkhani imene inali mʼkamwamʼkamwa kuyambira ku Galileya+ mpaka ku Yudeya konse, pambuyo pa ubatizo umene Yohane ankalalikira. 38 Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, amene Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Popeza Mulungu anali naye,+ anayenda mʼdziko lonse nʼkumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu onse amene Mdyerekezi+ ankawazunza.
-