9 Ndi ndani amene adzandibweretse kumzinda wozunguliridwa ndi adani?
Ndi ndani amene adzanditsogolere mpaka kukafika ku Edomu?+
10 Kodi si inu Mulungu amene munatikana,
Mulungu wathu, amene simukutsogoleranso magulu athu ankhondo?+
11 Tithandizeni pamene tikukumana ndi mavuto,
Chifukwa chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake.+
12 Mulungu adzatipatsa mphamvu,+
Ndipo adzapondaponda adani athu.+