10 Ndi ndani amene adzandibweretse kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri?
Ndi ndani amene adzanditsogolere mpaka kukafika ku Edomu?+
11 Kodi si inu Mulungu amene munatikana,
Mulungu wathu, amene simukutsogoleranso magulu athu ankhondo?+
12 Tithandizeni pamene tikukumana ndi mavuto,+
Chifukwa chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake.+
13 Mulungu adzatipatsa mphamvu,+
Ndipo adzapondaponda adani athu.+