-
Salimo 1:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Koma amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova,+
Ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama* chilamulocho masana ndi usiku.+
3 Iye adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa ngalande za madzi,
Umene umabereka zipatso mʼnyengo yake,
Umenenso masamba ake safota.
Ndipo zonse zimene amachita zimamuyendera bwino.+
-