-
Yesaya 40:26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 “Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone.
Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi?+
Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezi ndipo zonse amaziwerenga.
Iliyonse amaiitana poitchula dzina lake.+
Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu,+
Palibe iliyonse imene imasowa.
-
-
Aheberi 11:33, 34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu amenewa anagonjetsa maufumu pankhondo,+ anachita chilungamo, analonjezedwa zinthu zina+ ndiponso anatseka mikango pakamwa.+ 34 Sanapse ndi moto,+ sanaphedwe ndi lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ anamenya nkhondo mwamphamvu+ ndiponso anathamangitsa magulu ankhondo.+
-