Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 10:8-14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: “Usawaope,+ chifukwa ndawapereka mʼmanja mwako.+ Ndipo palibe aliyense amene adzatha kulimbana nawe.”+ 9 Yoswa anayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, ndipo anafika kwa adaniwo modzidzimutsa. 10 Yehova anasokoneza adaniwo pamaso pa Aisiraeli.+ Ndipo Aisiraeli anapha adani ambirimbiri ku Gibiyoni. Anawathamangitsa kulowera kuchitunda cha Beti-horoni ndipo anapitiriza kuwapha mpaka kukafika ku Azeka ndi ku Makeda. 11 Atafika pamalo otsetsereka otchedwa Beti-horoni pothawa Aisiraeli, Yehova anayamba kuwagwetsera matalala akuluakulu mpaka kukafika ku Azeka ndipo adaniwo ankafa. Amene anaphedwa ndi matalalawo anali ambiri kuposa amene Aisiraeli anawapha ndi lupanga.

      12 Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori kwa Aisiraeli, mʼpamene Yoswa analankhula ndi Yehova pamaso pa Aisiraeli kuti:

      “Dzuwa, ima+ pamwamba pa Gibiyoni,+

      Ndipo mwezi, uime pamwamba pa chigwa cha Aijaloni.”

      13 Choncho dzuwa linaimadi, ndiponso mwezi sunayende mpaka mtunduwo utalanga adani ake. Kodi sizinalembedwe mʼbuku la Yasari?+ Dzuwa linaima kumwamba pakatikati, ndipo linaimabe choncho pafupifupi maola 24.* 14 Palibe tsiku ngati limeneli, kaya pambuyo pake kapena patsogolo pake, limene Yehova anamvera mawu a munthu mʼnjira imeneyi,+ popeza Yehova anamenyera nkhondo Isiraeli.+

  • 2 Samueli 5:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero anati: “Yehova wayenda patsogolo panga ngati madzi a chigumula nʼkuwononga adani anga.”+ Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Baala-perazimu.*+

  • 1 Mbiri 14:10-16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Ndiyeno Davide anafunsira kwa Mulungu kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anauza Davide kuti: “Pita, amenewa ndiwaperekadi mʼmanja mwako.”+ 11 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Ndiyeno Davide anati: “Mulungu woona wawononga adani anga ngati madzi achigumula pogwiritsa ntchito dzanja langa.” Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Baala-perazimu.* 12 Afilisiti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide atalamula, milunguyo anaitentha pamoto.+

      13 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso nʼkuyamba kuukira anthu okhala mʼchigwacho.+ 14 Ndiyeno Davide anafunsiranso kwa Mulungu ndipo Mulungu woonayo anamuyankha kuti: “Usapite kukakumana nawo. Uwazembere kumbuyo nʼkuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 15 Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za bakazo, ukatuluke nʼkuyamba kumenyana nawo chifukwa Mulungu woona adzakhala atatsogola kukapha asilikali a Afilisiti.”+ 16 Choncho Davide anachitadi zimene Mulungu woona anamulamula,+ moti iwo anapha asilikali a Afilisiti kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena