-
Salimo 80:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Inu Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, chonde bwererani.
Yangʼanani pansi pano muli kumwambako kuti muone,
Ndipo samalirani mtengo wa mpesa uwu,+
15 Mtengo umene dzanja lanu lamanja ladzala.+
Ndipo muone mwana wanu amene munamupatsa* mphamvu kuti inu mulemekezeke.+
16 Wawotchedwa ndi moto+ nʼkudulidwa.
Anthu amawonongeka ndi kudzudzula kwanu.*
-
-
Ezekieli 20:47Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Uuze nkhalango yakumʼmwerayo kuti, ‘Imva mawu a Yehova. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikukuyatsa ndi moto.+ Motowo udzawotcha mtengo uliwonse wauwisi ndi mtengo uliwonse wouma umene uli mwa iwe. Malawi a motowo sadzazimitsidwa+ ndipo nkhope iliyonse, kuchokera kumʼmwera mpaka kumpoto idzapsa ndi moto.
-