-
Yesaya 49:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Ngakhale kuti malo ako anawonongedwa komanso kusakazidwa ndipo dziko lako linali mabwinja,+
Tsopano anthu amene adzakhale mmenemo malo adzawachepera moti adzakhala mopanikizana,+
20 Ana ako amene unabereka ana ena onse atamwalira, adzakuuza kuti,
‘Malowa atichepera.
Tipezereni malo oti tizikhalamo.’+
-
-
Yesaya 54:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
54 “Fuula mosangalala iwe mkazi amene sunaberekepo mwana.+
Iwe amene sunamvepo zowawa za pobereka,+ sangalala ndipo ufuule mosangalala.+
Chifukwa ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri
Kuposa ana a mkazi yemwe ali ndi mwamuna,”*+ akutero Yehova.
Tambasula nsalu za chihema chako chachikulu.
Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za tenti yako
Ndipo ulimbitse zikhomo zake.+
-