-
Mateyu 3:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Mʼmasiku amenewo, Yohane+ Mʼbatizi anapita mʼchipululu cha Yudeya nʼkuyamba kulalikira.+ 2 Iye ankalalikira kuti: “Lapani, chifukwa Ufumu wakumwamba wayandikira.”+ 3 Mneneri Yesaya ananeneratu za iyeyu+ mʼmawu awa: “Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.’”+
-
-
Maliko 1:2-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼbuku la mneneri Yesaya kuti: “(Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole* kukakukonzera njira.)*+ 3 Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.’”+ 4 Yohane Mʼbatizi anali mʼchipululu ndipo ankalalikira za ubatizo monga chizindikiro cha kulapa kuti machimo akhululukidwe.+
-