Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 12:9-14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Atachoka malo amenewo, anakalowa musunagoge wawo. 10 Mmenemo munali munthu wolumala dzanja.+ Choncho iwo anamufunsa kuti, “Kodi nʼzololeka kuchiritsa odwala pa tsiku la Sabata?” Cholinga chawo chinali choti amupezere chifukwa nʼkumuimba mlandu.+ 11 Koma iye anawayankha kuti: “Mutakhala ndi nkhosa imodzi yokha, ndiyeno nkhosayo nʼkugwera mʼdzenje pa tsiku la Sabata, kodi alipo pakati panu amene sangaigwire nʼkuitulutsa?+ 12 Komatu munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa! Choncho ndi zololeka kuchita chinthu chabwino pa tsiku la Sabata.” 13 Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhalanso bwinobwino ngati linzake. 14 Koma Afarisiwo anatuluka nʼkukakonza chiwembu kuti amuphe.

  • Luka 6:6-11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tsiku linanso la sabata,+ iye analowa musunagoge nʼkuyamba kuphunzitsa. Mmenemo munali munthu amene dzanja lake lamanja linali lolumala.+ 7 Alembi ndi Afarisi ankamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa Sabata nʼcholinga choti amuimbe mlandu. 8 Koma iye anadziwa zimene iwo ankaganiza.+ Choncho anauza munthu wolumala dzanjayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.” Munthuyo ananyamuka nʼkuima pamenepo. 9 Kenako Yesu anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiyani pa Sabata, chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ 10 Atayangʼana uku ndi uku, anauza munthu uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhalanso labwinobwino. 11 Koma iwo anakwiya kwambiri ndipo anayamba kukambirana zoti amuchite Yesu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena