Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mateyu 12:24-30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Afarisi atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi koma ndi mphamvu za Belezebule,* wolamulira ziwanda.”+ 25 Atadziwa maganizo awo, iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo mzinda kapena nyumba iliyonse yogawanika sikhalitsa. 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagawanika. Nanga tsopano ufumu wake ungakhalepo bwanji? 27 Komanso ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule, nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Nʼchifukwa chake otsatira anuwo adzakuweruzani kuti ndinu olakwa. 28 Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikirani modzidzimutsa.+ 29 Kapena munthu angalowe bwanji mʼnyumba ya munthu wamphamvu nʼkumulanda katundu wake, ngati choyamba atapanda kumanga munthu wamphamvuyo? Akatero mʼpamene angathe kutenga katundu mʼnyumbamo. 30 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine ndipo amene sagwira ntchito yosonkhanitsa anthu limodzi ndi ine amawabalalitsa.+

  • Maliko 3:22-27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Komanso alembi amene anachokera ku Yerusalemu ankanena kuti: “Ali ndi Belezebule,* ndipo amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 23 Choncho atawaitana, anayankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo kuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu wagawanika, ufumu umenewo sungakhalitse.+ 25 Ndiponso ngati nyumba yagawanika, nyumba yoteroyo singakhalitse. 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana wadziukira yekha ndipo wagawanika, sangakhalitse koma akupita kokatha. 27 Kunena zoona, palibe amene angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu nʼkuba katundu wake ngati choyamba atapanda kumanga munthu wamphamvuyo. Akatero mʼpamene angathe kutenga katundu mʼnyumbamo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena