-
Mateyu 12:24-29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Afarisi atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi koma ndi mphamvu za Belezebule,* wolamulira ziwanda.”+ 25 Atadziwa maganizo awo, iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo mzinda kapena nyumba iliyonse yogawanika sikhalitsa. 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagawanika. Nanga tsopano ufumu wake ungakhalepo bwanji? 27 Komanso ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule, nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Nʼchifukwa chake otsatira anuwo adzakuweruzani kuti ndinu olakwa. 28 Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikirani modzidzimutsa.+ 29 Kapena munthu angalowe bwanji mʼnyumba ya munthu wamphamvu nʼkumulanda katundu wake, ngati choyamba atapanda kumanga munthu wamphamvuyo? Akatero mʼpamene angathe kutenga katundu mʼnyumbamo.
-