-
Maliko 3:22-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Komanso alembi amene anachokera ku Yerusalemu ankanena kuti: “Ali ndi Belezebule,* ndipo amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 23 Choncho atawaitana, anayankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo kuti: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? 24 Ngati ufumu wagawanika, ufumu umenewo sungakhalitse.+ 25 Ndiponso ngati nyumba yagawanika, nyumba yoteroyo singakhalitse. 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana wadziukira yekha ndipo wagawanika, sangakhalitse koma akupita kokatha. 27 Kunena zoona, palibe amene angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu nʼkuba katundu wake ngati choyamba atapanda kumanga munthu wamphamvuyo. Akatero mʼpamene angathe kutenga katundu mʼnyumbamo.
-
-
Luka 11:15-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Koma ena mwa iwo ananena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule,* wolamulira ziwanda.”+ 16 Koma ena pofuna kumuyesa, anayamba kumukakamiza kuti awasonyeze chizindikiro+ chochokera kumwamba. 17 Atadziwa maganizo awo,+ iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo nyumba yogawanika imagwa. 18 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana nayenso wagawanika, kodi ufumu wake ungakhalepo bwanji? Chifukwa inu mukunena kuti ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule. 19 Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebule, nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Nʼchifukwa chake otsatira anuwo adzakuweruzani kuti ndinu olakwa. 20 Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu,+ ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikirani modzidzimutsa.+ 21 Munthu wamphamvu amene ali ndi zida zokwanira, akamalondera nyumba yake, chuma chake chimatetezeka. 22 Koma wina wamphamvu kuposa iyeyu akabwera nʼkumugonjetsa, amamulanda zida zake zonse zimene amadalira ndipo katundu amene wamulanda, amamugawa kwa ena. 23 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine ndipo amene sagwira ntchito yosonkhanitsa anthu limodzi ndi ine amawabalalitsa.+
-