Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Miyambo 15:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Kuyankha modekha* kumabweza mkwiyo,+

      Koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+

  • Agalatiya 6:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Abale, ngati munthu wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu amene ndi oyenerera mwauzimu, yesani kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Koma pamene mukuchita zimenezi musamale,+ kuopera kuti inunso mungayesedwe.+

  • Aefeso 4:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Choncho ine, amene ndili mʼndende+ chifukwa cha Ambuye, ndikukuchondererani kuti muzichita zinthu mogwirizana+ ndi kuitana kumene anakuitanani. 2 Nthawi zonse muzichita zinthu modzichepetsa,*+ mofatsa, moleza mtima+ ndiponso muzilolerana chifukwa cha chikondi.+

  • 1 Timoteyo 6:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi. Mʼmalomwake yesetsa kukhala wachilungamo, wodzipereka kwa Mulungu, wachikhulupiriro, wachikondi, wopirira ndiponso wofatsa.+

  • 2 Timoteyo 2:24, 25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu. Koma ayenera kukhala wodekha kwa onse,+ woyenerera kuphunzitsa, wougwira mtima ena akamulakwira+ 25 ndiponso wotha kulangiza mofatsa anthu otsutsa+ kuti mwina Mulungu angawalole kulapa* nʼkudziwa choonadi molondola.+

  • 1 Petulo 3:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena