-
Aheberi 10:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Munthu aliyense amene wanyalanyaza Chilamulo cha Mose amafa popanda kumuchitira chifundo, ngati anthu awiri kapena atatu apereka umboni.+ 29 Ndiye kuli bwanji munthu amene wapondaponda Mwana wa Mulungu, amene akuona magazi a pangano amene anayeretsedwa nawo ngati chinthu wamba,+ amenenso wanyoza mzimu umene Mulungu amasonyezera kukoma mtima kwakukulu?+ Munthu ameneyu akuyenera kulandira chilango chachikulu kwambiri.
-