-
Numeri 14:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Komabe anthu onse amene aona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, komanso zimene ndachita mʼchipululu, koma apitiriza kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, ndipo sanamvere mawu anga,+ 23 sadzaliona mʼpangʼono pomwe dziko limene ndinalumbirira makolo awo. Ndithudi, onse amene sakundipatsa ulemu, sadzaliona dzikolo.+
-
-
Numeri 14:28-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzakuchitirani mogwirizana ndi zimene ndamva mukulankhula.+ 29 Mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ 30 Nonsenu simudzalowa mʼdziko limene ndinalumbira* kuti mudzakhalamo,+ kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+
-