Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+
75 Timakuyamikani, inu Mulungu, timakuyamikani.
Dzina lanu lili pafupi ndi ife,+
Ndipo anthu akulengeza ntchito zanu zodabwitsa.
2 Inu mukuti: “Ndikasankha nthawi yoti ndiweruze,
Ndimaweruza mwachilungamo.
3 Pamene dziko lapansi ndi onse okhala mmenemo ananjenjemera* ndi mantha,
Ine ndi amene ndinalimbitsa zipilala zake.” (Selah)
4 Anthu odzitukumula ndinawauza kuti, “Musadzitukumule,”
Ndipo oipa ndinawauza kuti, “Musadzikuze chifukwa choti muli ndi mphamvu.*
6 Chifukwa ulemu wa munthu suchokera
Kumʼmawa, kumadzulo kapena kumʼmwera.
Amatsitsa munthu wina nʼkukweza wina.+
Ndithudi, iye adzakhuthula vinyo yense
Ndipo anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa mpaka kugugudiza nsenga zake.”+
9 Koma ine ndidzalengeza zimenezi mpaka kalekale.
Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobo.