-
Yeremiya 25:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Yehova Mulungu wa Isiraeli anandiuza kuti: “Tenga kapu iyi ya vinyo wa mkwiyo imene ili mʼdzanja langa ndipo ukamwetse mitundu yonse imene ndikukutumizako.
-
-
Yeremiya 25:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Ngati angakakane kulandira kapuyi mʼmanja mwako kuti amwe, ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mukuyenera kumwa basi.
-
-
Chivumbulutso 14:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Mngelo wina wachitatu anawatsatira ndipo ankanena mofuula kuti: “Ngati wina walambira chilombo+ ndi chifaniziro chake ndipo walandira chizindikiro pachipumi kapena padzanja lake,+ 10 adzamwanso vinyo wosasungunula wa mkwiyo wa Mulungu amene akuthiridwa mʼkapu ya mkwiyo wake.+ Ndipo adzazunzidwa ndi moto ndi sulufule+ pamaso pa angelo oyera komanso pamaso pa Mwanawankhosa.
-