Nyimbo ya Solomo
6 “Kodi wachikondi wako wapita kuti,
Iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse?
Kodi wachikondi wako wadzera njira iti?
Tiye tikuthandize kumufunafuna.”
2 “Wachikondi wanga wapita kumunda wake,
Kumabedi amʼmunda a mbewu zonunkhira,
Kuti akadyetse ziweto kuminda,
Ndiponso kuti akathyole maluwa.+
Iye akudyetsera ziweto msipu umene uli pakati pa maluwa.”+
4 “Wokondedwa wangawe,+ ndiwe wokongola ngati Tiriza,*+
Ndiwe wooneka bwino ngati Yerusalemu,+
Ndipo ndiwe wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera.+
Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi
Zimene zikuthamanga potsika mapiri a ku Giliyadi.+
6 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa
Zimene zikuchokera kosambitsidwa,
Zonse zabereka mapasa,
Ndipo palibe imene ana ake afa.
9 Koma mmodzi yekha ndi amene ali njiwa yanga,+ wopanda chilema.
Iye ndi mwana wapadera kwambiri kwa mayi ake.
Ndi mwana amene amakondedwa ndi* mayi amene anamubereka.
Ana aakazi akamuona, amamunena kuti ndi wosangalala.
Mafumukazi ndi adzakazi amamutamanda.
10 ‘Kodi mkazi amene akuwala* ngati mʼbandakuchayu ndi ndani,
Amene ndi wokongola ngati mwezi wathunthu,
Wosadetsedwa ngati kuwala kwa dzuwa,
Wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera?’”+
11 “Ine ndinapita kumunda wa mitengo ya zipatso zokhala ndi mtedza,+
Kuti ndikaone ngati yaphuka masamba atsopano mʼchigwa,*
Kuti ndikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,
Ndiponso ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.
12 Mosazindikira,
Chifukwa cholakalaka kuona zinthu zimenezi, ndinakafika
Kumene kunali magaleta a anthu olemekezeka* a mtundu wanga.”
13 “Bwerera, bwerera iwe Msulami!
Bwerera, bwerera
Kuti tione kukongola kwako!”
“Nʼchifukwa chiyani mukuyangʼanitsitsa Msulami?”+
“Iye ali ngati gule wa magulu awiri a anthu.”*