Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Sauli anatumiza anthu kukadikirira nyumba yake kuti amuphe.+
3 Inu Yehova, taonani! Iwo amandidikirira panjira.+
Anthu amphamvu amandiukira
Koma osati chifukwa chakuti ndapanduka kapena kuchita tchimo lililonse.+
4 Ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse, iwo akuthamanga ndipo akukonzekera kundiukira.
Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.
5 Chifukwa inu Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, ndinu Mulungu wa Isiraeli.+
Nyamukani ndipo muone zimene mitundu yonse ya anthu ikuchita.
Musasonyeze chifundo kwa aliyense woipa komanso wachiwembu.+ (Selah)
7 Tamverani zimene zikutuluka pakamwa pawo.
Milomo yawo ili ngati malupanga,+
Chifukwa iwo akuti: “Ndani akumvetsera?”+
10 Mulungu amene amandisonyeza chikondi chokhulupirika adzandithandiza.+
Mulungu adzachititsa kuti ndione adani anga atagonja.+
11 Musawaphe, kuti anthu a mtundu wanga asaiwale.
Ndi mphamvu zanu achititseni kuti aziyendayenda,
Achititseni kuti agwe, inu Yehova, chishango chathu.+
12 Chifukwa cha tchimo lapakamwa pawo ndi mawu a milomo yawo,
Ndiponso chifukwa cha mawu otukwana komanso achinyengo amene amalankhula,+
Akodwe ndi kunyada kwawoko.
13 Muwawononge onse mutakwiya.+
Muwawononge kuti asakhaleponso.
Muwadziwitse kuti Mulungu akulamulira mbadwa za Yakobo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ (Selah)
16 Koma ine, ndidzaimba za mphamvu zanu.+
Mʼmawa ndidzanena mosangalala za chikondi chanu chokhulupirika.