Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g87 12/8 tsamba 11-12
  • Mtendere wa Dziko Lonse—Motani Ndipo Liti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtendere wa Dziko Lonse—Motani Ndipo Liti?
  • Galamukani!—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yophunzitsa ya Dziko Lonse
  • Tidzayenda M’dzina la Yehova Mpaka Muyaya!
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mtendere—Zenizenizo
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mmene Dziko Lidzagwirizanitsidwira
    Galamukani!—1994
  • Kodi Zidzatheka Bwanji Kuti Padziko Lonse Lapansi Padzakhale Mtendere?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—1987
g87 12/8 tsamba 11-12

Mtendere wa Dziko Lonse—Motani Ndipo Liti?

MTENDERE wa dziko lonse uli limodzi la maloto okondedwa kwambiri a mtundu wa anthu. Koma kulingalira kuti maboma a anthu angafikire iwo kuli chabe masomphenya. Maphunziro a mbiri yakale akuvomereza chimene Baibulo motsimikizirika limachitira umboni kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

Kokha Mlengi wamphamvuyonse wa chilengedwe, Yehova Mulungu, angabweretse mtendere wosatha. Ndipo iye wapereka lonjezo lake kuti adzachita tero. Motani? Osati kupyolera m’zoyesayesa za anthu koma kupyolera mwa zimene Yesu Kristu anapanga mutu wa kuphunzitsa kwake konse—Ufumu wa Mulungu wa kumwamba. (Mateyu 6:9, 10) Wolamulira wa Ufumu umenewo, Kristu Yesu, akutchedwa mu ulosi “Kalonga wa Mtendere” wowona. (Yesaya 9:6) Ndipo lonjezo la Mulungu liri lakuti pansi pa ulamuliro wa Ufumuwo, padzakhala “mtendere wochuluka” m’dziko lonse lapansi.—Masalmo 72:7.

Komabe, Baibulo momvekera bwino limasonyeza kuti chimenecho chisanachitike, dongosolo iri la zinthu la nkhondo liyenera kuchotsedwapo. (1 Yohane 2:15-17) Ndipo ulosi wa Baibulo umasonyeza kuti chiwonongeko chake chiri pafupi.—Mateyu 24:3-14, 22, 34; Luka 21:25-28; 2 Timoteo 3:1-5.

Ichi, chotero, chiri chifuno chosasinthika cha Mulungu “amene sakhoza kunama.” (Tito 1:2) Chotero, kodi atsogoleri a zipembedzo, makamaka awo a m’Dziko la Chipembedzo, sanapereke mapemphero m’chigwirizano ndi chifuno chimenechi? Kodi iwo sanachite zinthu m’chigwirizano ndi chifuno chimenecho? Komabe, palibe ndi mmodzi yense wa oimira a zipembedzo pa Assisi amene anatchula chirichonse ponena za kuyandikira kwa mapeto a dongosolo iri ndi kudza kwa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, uthenga weniweni wa Yesu ndi Mawu a Mulungu.

Ichi nchosadabwitsa chifukwa zipembedzo zimenezo sizinaphunzitse otsatira awo chowonadi ponena za zifuno za Mulungu. M’malo mwake, iwo ali mbali ya dziko iri lomwe liri pansi pa Satana, ndipo amalunjikitsa zoyesayesa zawo pa kulipititsa patsogolo ilo. Monga chotulukapo chake, anthu awo akhala ogawanikana, akumaika chikhulupiriro chokulira mu utundu m’malo mwa Ufumu wa Mulungu. Ichi chatsogolera iwo kuphana wina ndi mnzake m’kukangana kwa dziko lino. Chotero, mawu awa amagwira ntchito kwa zipembedzo zoterozo: “Akazi achigololo inu, kodi simudziŵa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.”—Yakobo 4:4.

Chotero, mapembedzero kaamba ka mtendere ochitidwa ndi zipembedzo zimenezi amagwera ku makutu ogontha. Iwo amabweretsa ku malingaliro mkhalidwe wa m’nthaŵi ya mneneri Yeremiya. Kubwerera m’nthaŵi imeneyo aneneri a zipembedzo zonyenga ananena kuti: “Mtendere! Mtendere!” Koma, m’chenicheni, ‘panalibe mtendere’ kwa iwo.—Yeremiya 6:14.

Ntchito Yophunzitsa ya Dziko Lonse

Komabe, chifuno cha Mulungu chidzakwaniritsidwa. (Yesaya 55:11) Chotero lerolino ntchito yophunzitsa Baibulo ya dziko lonse iri mkati. Ichi chiri m’chigwirizano ndi ulosi wa pa Mateyu 24:14, pamene pamanena kuti: “Ndipo mbiri yabwino imeneyi ya Ufumu idzalalikidwa pa dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo kenaka chidzafika chimaliziro, NW.”

Popeza awo amene ali mbali ya machitachita a dziko lonse lapansi amenewa a alambiri owona amagonjera ku zifuno za Mulungu, iwo achotsa zisonkhezero zogawanitsa za utundu pakati pawo. Iwo akhala chitaganya cha mtendere cha anthu omwe amakondana wina ndi mnzake ndi amene amakhalira moyo kaamba ka Ufumu wa Mulungu. Monga chotulukapo, iwo akukwaniritsa ulosi wochititsa nthumazi pa Mika 4, umene umati:

“Koma kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova [kulambira kwake kowona] lidzakhazikika pamwamba pa mapiri [mitundu ina yonse ya kulambira], . . . ndi mitundu ya anthu idzayendako. Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati: ‘Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ndi ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo, kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m’mabande ake.’ . . . Ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo.”—Mika 4:1-3.

Chiri chodziŵikiratu mokulira kuti ulosi umenewu sungakhale unakwaniritsidwa ndi msonkhano wa pa Assisi. Awo amene akuyenda ku phiri lophiphiritsira la kulambira kowona ali anthu omwe akulangizidwa ndi Yehova m’njira zokonda mtendere ndipo amene akuyenda mogwirizana ndi chifuno chake ndi zifuno zake. Iwo ali osati anthu omwe amakhalirira m’zipembedzo zawo zakale, zogawanikana ndi ziphunzitso ndi machitachita otsutsana. M’malo mwake, iwo akusonkhanitsidwa pamodzi monga mmene Mika 2:12 ananeneratu: “Ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa pakati pa busa pawo.”

Chotulukapo cha ntchito yophunzitsa imeneyi chiri chakuti anthu oposa mamiliyoni atatu m’mbali zonse zadziko lapansi akhala alaliki a “mbiri yabwino ya ufumu.” Iwo akhala anthu a mtendere, ndipo pansi pa mkhalidwe uliwonse iwo sadzatenga moyo wa munthu mnzawo. Monga mmene Mika ananeneratu, iwo asula kale “malupanga awo kukhala zolimira . . . ; ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Ndipo mamiliyoni a anthu ena okondwerera kuzungulira padziko lapansi akuphunzitsidwa ndi iwo.

Mboni za Yehova zimayang’ana kutsogolo ku dziko latsopano logwirizanitsidwa mu limene Mika 4:4 adzakwaniritsidwa kulinga ku mtundu wonse wa anthu: “Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsya; pakuti pakamwa pa Yehova [wa kumwamba] wa makamu padanena.” Kenaka, mu versi 5, Mika akusonyeza kusiyana pakati pa awo amene amalambira unyinji wa milungu yonama ndi awo amene amalambira Mulungu yekha wowona, akumanena kuti: “Pakuti mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yonka muyaya.” Mwachiwonekere, dzina la Mulungu silinatchulidwe nkomwe pa Assisi. Ngakhale kuli tero, kodi inu simungakonde kuphunzira ponena za Mulungu ameneyu wa Baibulo? Mboni za Yehova zidzakhala zachimwemwe kukuthandizani inu mu ichi.

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi ndani amene kwenikwenidi asula malupanga awo kukhala zolimira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena