Lingaliro Labaibulo
Ndani Angatonthoze ‘Kulira kwa Njala’?
“BOMA silingatidyetse ife chifukwa chakuti tiri ambiri koposa,” mlimi wakuda wa m’dziko la chonde la kum’mwera kwa Africa anauuza Galamukani! “Kwa zaka ziŵiri,” iye analongosola tero, “dziko lathu lakhala liri louma. Mvula yakhala isakubwera. Ng’ombe zonse zinafa chifukwa cha njala ndi ludzu. Aliyense akulira ndi njala.”
Masiku ochepa pambuyo pake, mvula yonyowetsa inabweretsa mpumulo ku gawo limenelo. Koma kuchira kudzatenga nthaŵi yaitali, ndipo ‘kulira kwa njala’ kukupitirizabe ku mbali zina zokulira za Africa; ndipo njalanso siiri kokha ndi malire ku dziko limenelo. Molingana ndi The Hunger Primer, yofalitsidwa ndi Food for the Hungry, maiko 43 a ku Asia ndi Latin America ali ndi “kuperewera kwa chakudya kochulukira.”
Koma m’nthaŵi zaposachedwapa, chisamaliro cha dziko chinalunjikitsidwa pa njala ya mu Africa, chokhala ndi “Mamiliyoni 150 ali pa Ngozi” malinga ndi mutu waukulu mu The Times ya ku London. Oyimba mu Britain ndi United States asonkhanitsa mamiliyoni a mapaundi ndi madola kuthandiza anthu a chiAfrica a njala. Ochititsidwa mantha pa kuwona anthu ambiri akumafa ndi njala pa ma TV, mwinamwake munadabwa, ‘Nchifukwa ninji kuli njala?’
Kodi Tipatse Mlandu Nyengo?
“Unyinji suuli wokhutiritsidwa kotheratu ndi kuuzidwa kuti njala mu Africa imachititsidwa ndi chilala,” akulemba tero wotsogoza wa nkhani za m’malo otizinga pa Earthscan, mu magazini ya chiBritish ya People. Chifukwa ninji? Kaamba ka chinthu chimodzi, mu mazana apita chilala nthaŵi zonse sichinatulukepo m’tsoka.
Africa ali ndi nthaka yabwino ya kubzyala chakudya chokwanira chiŵerengero chake cha anthu choposa chimene chiripo. Koma dongosolo la chuma la dziko silikulimbikitsa ichi. Kugonjera kwa maboma ku chitsenderezo cha za chuma, anthu a m’mudzi olima akuchotsedwa kuchokera pa dziko la chonde—dziko limene tsopano likugwiritsiridwa ntchito kugawira misika ya kunja ndi chakudya ndi zinthu. Kudera nkhaŵa chotero kukufuulidwa kaamba ka anthu ambiri okhala m’midzi yosauka ya ku Africa, pamene ambiri akudabwa kuti kaya iwo adzapeza zokwanira kudya.
Mbali ina iri njira mmene maboma amagawirira chuma. “Mizinda kumene maboma amakhala,” akulongosola Lloyd Timberlake m’bukhu lake lakuti Africa in Crisis, “yapatukana kuchokera ku midzi, ndipo ndalama zogwiritsira ntchito ya chitukuko zagwiritsiridwa ntchito kudzaza mizinda imeneyo ndi mahotela, mafakitale, mayuniversite ndi magalimoto. Ichi chalipiridwa mwa kulanda anthu asanu ndi aŵiri pa anthu khumi a chiAfrica alionse okhala ku mudzi.”
Kodi Thandizo la Kunja Lingaletse ‘Kulira kwa Njala’?
“Panthaŵi imodzi imene dziko la kunja limapereka ndi dzanja limodzi, limatenganso ndi dzanja lina,” ikutero Famine: A Man-Made Disaster?, ripoti lochokera ku Independent Commission on International Humanitarian Issues. “Maboma othandizira,” ilo likupitiriza, “sayenera kusunga zinyengo. M’malo mwathandizolo kukhala laulere, maiko othandizira ayamba kuchita malonda.” Chifukwa ninji? Chifukwa maiko othandizira kaŵirikaŵiri amapeza zochuluka m’kubwezera ku thandizo loterolo. Africa, ikulongosola tero magazini ya chiBritish ya The Ecologists, “adakali magwero a akulu a zoperekedwa za mbewu zomwe timadya tsiku ndi tsiku mu UK. . . . [Alinso] wotulutsa wamkulu wa mpira, thonje, mitengo yolimba ya kumalo otentha, ndipo mowonjezereka akupititsidwa patsogolo monga magwero a ng’ombe, ndiwo za masamba ndi maluŵa awisi.”
Zowona, Africa amapeza ndalama kaamba ka zinthu zogulitsidwa kunja zonsezi, koma ndalama kaŵirikaŵiri sizigwiritsiridwa ntchito kuthandiza a njala. M’malo mwake, zikugwiritsiridwa ntchito kutukula mizinda, kupititsa patsogolo zinthu zogulitsa kunja, kugula zida za nkhondo, ndi kubwezera ngongole za thandizo za maiko akunja. “Chifukwa chakuti osauka akudyetsa olemera,” ikunena tero magazini ya U.S. The Nation, “njala mu mbali zambiri za dziko idzawonjezereka. . . . Katundu wogulitsidwa kunja wowonjezereka adzapereka phindu ku bizinesi ya zamalimidwe ya mitundu yonse, . . . koma sidzadyetsa anthu a ku Africa a njala.”
Boma Lodzatonthoza ‘Kulirako’
Njala ya mu Africa imawunikira chochitika chofala chakale. “Wina apweteka mnzake pomlamulira.” Kulongosola nchifukwa ninji chitsenderezo chimenecho chikupitiriza, Baibulo likunena kuti: “Chokhotakhota sichingawongokenso.” (Mlaliki 1:15; 8:9) Inde, maboma a anthu apangidwa ndi anthu opanda ungwiro omwe ali ndi zikhoterero za dyera. Ndimotani mmene makhazikitsidwe oterowo angakhalire “owongoka” ndipo mowona mtima kusamalira kaamba ka zosowa zadziko lapansi losauka?
Kaamba ka yankho, lingalirani mmene chilala chimodzi choipa kwambiri m’mbiri ya Africa chinalakidwira. Icho chinayamba chifupifupi 1730 B.C.E. ndipo chinatha zaka zisanu ndi ziŵiri. Koma wolamulira wa Igupto analandira chitsogozo chaumulungu mwa kusunga tirigu wambiri mkati mwa zaka zapitazo zabwino. Chifukwa cha ichi, palibe ndi mmodzi yemwe wa nzika zake amene akusimbidwa kukhala anafa ndi njala. M’chenicheni, anthu ochokera ku maiko ena anabwera kudzagula chakudya kuchokera ku Igupto chifukwa “njala inakula m’dziko lonse lapansi.”—Genesis 41:1-57; 47:13-26.
Ndi kwa ndani kumene chitsogozo chaumulungu chikuloza lerolino? Kwa amene akuwalitsa chiyembekezo ku mbiri yomvetsa chisoni ya munthu ya chitsenderezo ndi yokhotakhota—Yesu Kristu. “Anapitapita [m’dziko, NW] nachita zabwino,” Baibulo likusimba tero. “Iye [sanachite chimo, NW].” (Machitidwe 10:38; 1 Petro 2:22) ‘Koma,’ inu mungafunse, ‘kodi chimenechi chiri ndi chiyani chochita ndi boma limene lingatonthoze “kulira kwa njala”?’ Zambiri koposa chifukwa Yesu ali woikidwa ndi Mulungu kukhala Wolamulira pa mtundu wonse wa anthu. Zabwino zonse zimene Yesu anachita, kuphatikizapo kudyetsa mozizwitsa khamu la njala, zinasonyeza upamwamba wa Ufumu wa kumwamba wa Mulungu pa maboma a anthu aliwonse. Iye analozanso kutsogolo ku nthaŵi pamene Ufumu wa Mulungu udzatenga ulamuliro pa dziko lonse lapansi.—Marko 8:1-9; Chivumbulutso 11:15.
Mwamsanga, Wolamulira woikidwa wa Mulungu adzawona ku kugawiridwa koyenera kwa chakudya. Iye angatonthoze ‘kulira kwa njala.’ (Luka 21:10, 11, 31) Baibulo lirinso ndi lonjezo lotonthoza mtima ponena za ulamuliro wa Kristu: “Ndipo adzachita ufumu kuchokera kunyanja kufikira kunyanja . . . kufikira malekezero a dziko lapansi. Adzachitira chisoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. M’dzikomo mudzakhala dzinthu zochuluka pamwamba pa mapiri.” Mkati mwanthaŵi imeneyo palibe wina aliyense akafunikira kunena kuti, “Boma silingatidyetse ife,” popeza njala, limodzi ndi kuvutika ndi imfa, sizidzakhalako.—Masalmo 72:8, 13, 16; Chivumbulutso 21:3-5.
[Chithunzi patsamba 18]
Dziko lapansi limatulutsa chakudya chambiri