Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 5/8 tsamba 20-22
  • “Lemekeza Atate Wako ndi Amako”—Koma Nchifukwa Ninji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Lemekeza Atate Wako ndi Amako”—Koma Nchifukwa Ninji?
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi “Kulemekeza” Kumatanthauzanji?
  • Nchifukwa Ninji Mufunikira Kulemekeza Makolo Anu?
  • Makolo a Vuto
  • ‘Chimene Atate Anga Ananena Chinali Cholondola’
  • Chitirani Ulemu Anthu Onse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • “Uzilemekeza Bambo Ako ndi Mayi Ako”
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Kodi Munthu Angasonyeze Bwanji Kuti ‘Amalemekeza Bambo Ake ndi Mayi Ake’?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Ndingatani Makolo Anga Akamakangana?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 5/8 tsamba 20-22

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

“Lemekeza Atate Wako ndi Amako”—Koma Nchifukwa Ninji?

“NDIWE wowuma mutu kwenikweni kotero kuti sindingachite chirichonse ndi iwe,” anatero atate okwiyitsidwa a Veda. “Iwe sumandipatsa ine ulemu. Ukufunsa kaamba ka mavuto.” Veda ankapita kocheza ndi mnyamata yemwe ankagwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa. Iye kaŵirikaŵiri ankavina kufikira maora a mmawa kwenikweni. Ngakhale kuti atate wake anachitsutsa icho mokulira, Veda sanasamale.

“Ndinadzimva kuti iwo anali oletsa kwambiri,” analongosola tero Veda. “Panthaŵi imeneyo ndinali wa zaka zakubadwa 18, ndipo ndinalingalira kuti ndinali wachikulire ndipo ndinadziŵa zonsezo. Ndinadzimva kuti atate anga anali onkitsa ndipo sanangofuna kuti ine ndikhale ndi nthaŵi yabwino, chotero ndinapita kunja ndi kuchita zomwe ndinafuna kuchita.”

Wachichepere wina, Gina, analemba kuti: “Atate anga ankaledzera kwambiri, ndipo sindinakhoze kugona chifukwa chakuti makolo anga ankakalipirana ndi kufuula kwambiri. Ndinangokhala pa kama wanga ndi kungolira. Sindinakhoze kuwawuza iwo mmene ndinadzimverera ponena za icho chifukwa chakuti amayi anga mwinamwake akanandimenya ine. Baibulo limanena kuti ‘lemekeza atate wako,’ koma sindingakhoze.”

Mwinamwake, mofanana ndi Veda ndi Gina, inu mumachipeza kukhala chovuta kulemekeza makolo anu. Chingakhale chifukwa chakuti iwo akupanga chimene inu mumadzimva kukhala zifuno zopanda kulingalira kapena akusonyeza chitsanzo choipa m’mikhalidwe. Komabe, Baibulo limalamula momvekera bwino: “Lemekeza atate wako ndi amako.” (Aefeso 6:2) Kodi ichi chimaphatikizapo chiyani? Ndipo kodi pali zifukwa zabwino za kuchitira tero, ngakhale ngati makolo apangitsa kuwalemekeza kukhala kovuta?

Kodi “Kulemekeza” Kumatanthauzanji?

“Kulemekeza” kumaphatikizapo kuzindikira kwa ulamuliro woikidwa mwa lamulo. Mwachitsanzo, Akristu amalamulidwa, “Chitirani mfumu ulemu.” (1 Petro 2:17) Pamene kuli kwakuti inu simungavomerezane nthaŵi zonse ndi wolamulira wa dziko, malo ake kapena kagwiridwe ka ntchito kafunikira kulemekezedwabe. Mu mbali ya banja, Mulungu anaveka makolo ndi ulamuliro winawake monga omuimira ake. Chotero, ana aumulungu afunikira kulemekeza ulamuliro umenewo. Koma ana adzafunikira kusonyeza zoposa kokha ulemu wamba.

Verebu la Chigriki loyambirira lolongosoledwa kukhala “kulemekeza” m’Baibulo kwakukulukulu limatanthauza kulingalira winawake kukhala wa mtengo waukulu. Chotero kholo lifunikira kuwonedwa monga la mtengo wapatali, lokwezedwa mokulira ndipo lokondedwa kwa inu. Ichi chimaphatikizapo kukhala ndi malingaliro otentha, oyamikira kaamba ka iwo. ‘Koma kodi ndimotani mmene ndingadzimverere mwanjirayo pamene kuli kwakuti iwo amandipatsa ine nthaŵi yovuta?’ mukufunsa tero.

Nchifukwa Ninji Mufunikira Kulemekeza Makolo Anu?

Popeza chinthu chimodzi, Miyambo 23:22 imanena kuti: “Tamvera atate wako anakubala, usapeputse amako.” Pali kuyerekezedwa kwa kuchotsa mimba 55 miliyoni kuzungulira dziko lonse chaka chirichonse. Chenicheni chokha chakuti makolo anu anakulolani inu kubadwa chiri chifukwa chimodzi cha kuwalemekezera iwo. Gregory, yemwe pa nthaŵi imodzi anali wopanda ulemu koposa, anadzazindikira chimenechi. “Ndinayamba kumvetsetsa chirichonse chimene amayi anachita kaamba ka ine,” iye akuvomereza tero. “Ndimayamikira Yehova Mulungu kuti iwo sanandiphe m’mimba kapena kunditaya ine m’chitini choponyera zinyalala monga khanda. Iwo ali kholo limodzi, ndipo pali asanu ndi mmodzi a ife. Ndikudziwa kuti chinali chovuta kwa iwo.”

Kulera ana, ngakhale ndi tero, sikuli kokha “kovuta” komanso kuli kodula. Ripoti la ku Canada linavumbula kuti zowonongedwa za kulera mwana kufika ku msinkhu wa 18 ndi banja la makolo aŵiri okhala kokha ndi mwana mmodzi ziri chifupifupi $66,400! Lingalirani ponena za kudzikana kwa makolo anu ndi cholinga cha kufuna kukupezerani chakudya ndi zovala. “Nthaŵi ina chokha chomwe chinatsala chakudya chinali chitini cha chimanga ndi zipatso zina,” analongosola tero Gregory. “Amayi anga anaziyika izo kaamba ka anafe, koma iwo sanadye. Ndinapita kukagona wokhuta, koma ndinapitirizabe kudabwa chifukwa chimene Amayi sanadyere. Tsopano popeza kuti ndiri ndi banja langa, ndimazindikira kuti iwo ankadzivutitsa kaamba ka ife. Ndikudabwa ngati ndingakhoze kupereka zakudya kaamba ka mwana wanga. Sindikuwona mmene iwo anachichitira icho.”

Mosakaikira, makolo anu anathanso usiku wochulukira osagona kusamalira kaamba ka inu pamene munadwala. Panali mateŵera mazana ochulukira ofunika kusinthidwa ndi unyinji wa zovala zanu zakuda zofunika kuchapa. Anthu a ku America oposa 200,000 anafunsidwa kulongosola kaya ndi ana angati omwe akafuna kukhala nawo ngati iwo akakhoza kuchichitanso. ‘Tikakhoza kukhala ndi chiŵerengero chimodzimodzicho,’ inalongosola tero 54 peresenti ya makolo! Kokha 6 peresenti ananena kuti, “Osati ndi mmodzi yemwe.”

Chotero makolo anu anakupatsani moyo ndi kukusamalirani inu. Motsimikizirika iwo amayenerera ulemu wanu ndi kulemekeza.

Makolo a Vuto

Bwanji, ngakhale ndi tero, ngati makolo anu amasonyeza chitsanzo choipa, mwinamwake kukhala okwiya, zidakwa, kapena amakhalidwe oipa? Momvekera, inu mungavutike monga chotulukapo. Kodi ndimotani mmene mungalemekezere makolo oterowo?a

Monga anthu opanda ungwiro, makolo anu angakhale ndi mavuto okulira kapena kusemphana kwaumunthu. (Mlaliki 7:20) Komabe, mosasamala kanthu za kuphophonya kwawo, Mulungu wawapatsa iwo mlingo wina wa kulamulira pa moyo wanu. Iye amakufunanibe inu kulemekeza ulamuliro wawo. Kumbukirani, Mulungu ananena kuti ulemu wofunika uyenera kusonyezedwa ngakhale kwa olamulira. (Aroma 13:7) Ichi chimafunikira kuyang’ana kupyola mkhalidwe wawo ndi kusumika pa ntchito yawo, kapena malo. Chotero m’malo mokhala wosalemekeza ngati mukudzimva kuti kholo likugwiritsira ntchito molakwa ulamuliro wake, yeserani kukhala chete. (Yerekezani ndi Mlaliki 10:4.) Siyani nkhaniyo m’manja mwa Mulungu, popeza kuti “iye wakuchita chosalungama adzalandira chosalungama anachichitacho, ndipo palibe tsankho.”—Akolose 3:25.

Inu muyenera kuyang’anizana ndi chenicheni chakuti malinga ngati kholo lanu likupereka zina zake kaamba ka inu, ilo liri ndi thayo kaamba ka banja. Mlaliki 8:3, 4 amalongosola kuti: “Pakuti iyeyo amachita chomwe chimukonda [yemwe ali ndi ulamuliro], pakuti mawu a mfumu ali ndi mphamvu.” Kuwukira kumakuikani inu m’mkhalidwe wa kusapambana.

Ndimotani, ngakhale ndi tero, mmene mungapewere kukulitsa kukalipitsidwa? Yeserani kumvetsetsa chifukwa chimene makolo anu amachitira m’njira imene akuchita. Ndiponso, zikumbutseni inu eni za mapindu omwe akupereka. Mwachitsanzo, Dody, yemwe anali ndi amayi okwiya msanga ndi atate opeza okonda zakumwa zoledzeretsa, analemba kuti: “Mwinamwake amayi anga sanakhoze kutisonyeza ife chikondi chifukwa chakuti, pokhala mwana woipsyidwa, iwo sanaphunzitsidwe mmene angachitire. Atate anga opeza anasonyeza chikondwerero m’zochitachita zathu pamene anali osaledzera, koma chimenecho sichinali cha kaŵirikaŵiri. Komabe, mng’ono wanga ndi ine nthaŵi zonse tinali ndi zofunda ndi zakudya m’chiwiya choziziritsira zinthu.” Chotero chikumbumtima cha Dody chiri changwiro, podziŵa kuti iye anachita chomwe anayenera kulemekeza makolo ake.

Kulemekeza winawake moyenerera sikumatanthauza kuti muvomerezane ndi iye. “Sunga mawu a mfumu [kapena kholo], makamaka m’kulambira Mulungu,” amalangiza tero Mlaliki 8:2. Malinga ngati lamulolo silikusemphana ndi malamulo a Mulungu, sonyezani chikondi chanu kaamba ka Mulungu mwa kulilemekeza ilo. “Mverani akukubalani inu mu zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.”—Akolose 3:20.

M’kuwonjezerapo, ngakhale ngati chitsanzo cha kholo chiri choipa, inu musatsirize kuti chirichonse chimene iwo adzakuwuzani chiri cholakwa. M’nthaŵi ya masiku a Yesu Kristu, atsogoleri a chipembedzo omwe anali ndi ulamuliro mwa kuphunzitsa Mawu a Mulungu anakhala oipa kwenikweni. Komabe, Yesu anawuza anthu kuti: “Zinthu zirizonse zimene iwo akuwuzani inu, chitani nimusunge koma musatsanza ntchito zawo.” (Mateyu 23:1-3, 25, 26) Mwakulemekeza uphungu woperekedwa m’Mawu a Mulungu, anthu akakhoza kudalitsidwa ndi Mulungu. Ichi chingakhalenso tero ndi inu mwakulemekeza uphungu waumulungu wochokera kwa makolo anu.

‘Chimene Atate Anga Ananena Chinali Cholondola’

Potsirizira pake, Veda anasintha mkhalidwe wake kulinga kwa makolo ake. Koma iye anaphunzira m’njira yovuta. Pamene ankayenda ndi bwenzi lake la chinyamata, lomwe linali losokonezeka ndi mbanje ndi mowa, galimoto linachoka mu msewu. Ilo linakagunda pa mtengo wa magetsi pa liŵiro la 97 km pa ora limodzi, womwe unasakaza galimotolo ndi kusiya Veda ali ndi chironda chachikulu pa mphumi pake. Iye anathaŵa kuchoka pa ngoziyo, sanapite ku chipatala kuti akamuthandize.

“Pamene makolo anga anafika ku chipatala,” anawulula tero Veda, “ndinawawuza iwo kuti chirichonse chimene atate ananena chinali cholondola ndi kuti ndinayenera kumvera nthaŵi yaitali kumbuyoko.” Kuyambira pamenepo kupitirizabe, Veda anali wogamulapo kulemekeza makolo ake. “Sichinali chopepuka,” iye anavomereza tero, “popeza kuti ndinakhumbabe kupita kukavina, ndipo chinakhoza kudzetsa kusungulumwa kwenikweni kukhala panyumba. Koma ndinafuna kukondweretsa Mulungu. Ndinapanga kuphophonya kokulira, ndipo kunali pafupi kuwononga moyo wanga, chotero ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize ine kusintha mkhalidwe wanga.”

Veda anapeza phunziro lofunika—kulemekeza ulamuliro woyenera. Kulephera kuphunzira ichi kwalepheretsa ambiri kupita patsogolo ku sukulu, kukhala ndi ntchito kapena kukhala ndi ukwati wa chimwemwe. “Kuphunzira kulemekeza atate anga, ngakhale pamene sichinali chopepuka, ndithudi kunandithandiza ine kugonjera kwa mwamuna wanga,” anavumbula tero Veda, yemwe tsopano ali wokwatiwa mwachimwemwe. Inde, ponse paŵiri unansi wosangalatsa ndi ena ndi chikumbumtima chabwino kulinga kwa Mulungu ziri mphatso zochokera m’kuphunzira kulemekeza makolo anu.

[Mawu a M’munsi]

a Nkhaniyi sikulozera ku mkhalidwe wosakhoza kupiririka kotheratu mu umene wachichepere wawunikiridwa ku kuipsyidwa kwa kuthupi kapena kwa kugonana. M’nkhani zoterozo, wachichepere angafunikire kufunafuna thandizo lochokera kwa akatswiri kunja kwa banja. Onani “Kugonana kwa Pachibale—Upandu Wobisika” m’kope lathu la February 8, 1981, Chingelezi.

[Chithunzi patsamba 21]

Kuwunikira pa zonse zomwe makolo anu achita kaamba ka inu mkati mwa zaka kuyenera kukusonkhezerani inu kuwale-mekeza iwo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena