Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 6/8 tsamba 9-10
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Dziko Lopanda Zida?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Dziko Lopanda Zida?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maziko Obisika Avumbulidwa
  • Kuchotsa Thayo la Zida Zankhondo
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhondo Yothetsa Ndhondo
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Mphamvu ya Munthu Ingaletse Iwo?
    Galamukani!—1989
  • Kulekeka kwa Zida za Nyukliya—Motani?
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 6/8 tsamba 9-10

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Dziko Lopanda Zida?

NDI mpumulo wotani nanga umene chikakhala ngati thayo lotsendereza la malonda a zida zankhondo linachotsedwa ndipo kuwunjikidwa kwa zida kwa dziko lonse kunathetsedwa! Ndi chiyembekezo chotani chomwe chiripo kaamba ka chochitika choterocho? Mbiri yakale imasonyeza kuti mitundu sidzachita chimenecho pa iyo yokha. M’kuwonjezerapo, zida zankhondo ziri kokha chizindikiro. Vuto liyenera kuthetsedwa pa maziko ake kotero kuti lithetsedwe kotheratu. Kodi maziko amenewo angapezedwe, ndipo ngati ndi tero, ndani yemwe angalithetse ilo?

Malonda a zida zankhondo amapeza chakudya chawo kuchokera ku limodzi la matemberero aakulu a mtundu wa munthu, nkhondo. Koma nkhondo sinakule kuchokera ku malonda a zida zankhondo. M’malomwake, malonda a zida zankhondo anakula kuchokera ku nkhondo. Chotero, kodi maziko a kuipa ayenera kupezeka mu nkhondo? Ayi, nkhondo iri kokha nthambi pa imene malonda a zida zankhondo akudalira. Kodi nthambi imeneyo imapeza kuti chakudya chake?

Kodi ndani yemwe ali ndi mphamvu ya kuyambitsa nkhondo? Malamulo onse amaika mphamvu yoteroyo m’manja mwa maboma awo, omwe kaŵirikaŵiri amayambitsa nkhondo kuti apititse patsogolo kapena kutetezera zikondwerero za mtundu. Maboma amachirikizidwa ndi anthu. Chotero vutolo liri logwirizana ndi dongosolo lonse la kachitidwe ka zinthu la munthu, losonkhezeredwa ndi utundu, udani wa zachuma, kulamulira gawo, ndi ufuko. Chotero, kodi dongosolo iri la kachitidwe ndilo maziko a vutolo? Ayi. Kusanthula kosamalitsa kudzasonyeza kuti dongosolo la kachitidwe loipa limeneli limapeza chakudya chake kuchokera ku maziko obisika, magwero amene anthu ambiri amawanyalanyaza.

Maziko Obisika Avumbulidwa

Maziko amenewo avumbulidwa m’Baibulo. Bukhu lakale limeneli limavumbula kuti cholengedwa champhamvu chauzimu, chosonkhezeredwa ndi kudzikuza, chinadzikweza icho chokha m’kutsutsana ndi Mulungu. (Yobu 1:6-12; 2:1-7) Iye akutchedwa Satana (kutanthauza, Mdani) Mdyerekezi (kutanthauza, Wabodza, Woneneza). Iye anayambitsa chimo ndi imfa m’banja la munthu. (Genesis 3:1-7) Chotero, iye akutchedwa “woipayo.” Iye anawuzira chiwukiro chakupha choyamba m’mbiri yakale ya munthu, chija cha Kaini pa Abele.—1 Yohane 3:12; Genesis 4:8.

Baibulo limavumbulanso Satana monga “mulungu wa dongosolo lino la zinthu,” “chinjoka” chachikulu yemwe ‘akupereka mphamvu, mpando wachifumu, ndi ulamuliro waukulu’ ku dongosolo lolamulira la dziko lonse la ndale zadziko. Yesu Kristu molimba mtima analoza kuti “Mdyerekezi . . . anali wambanda kuyambira pachiyambi” ndi kumulongosola iye monga “wolamulira wa dziko.”—2 Akorinto 4:4, NW; Chibvumbulutso 12:9; 13:1, 2; Yohane 8:44; 14:30, NW.

Ngakhale kuli tero, maziko akupha amenewa sadzakhala kosatha. Kuphunzira Baibulo kumazindikiritsa nyengo yowopsya iripoyi mu mbiri yakale ya munthu monga masiku omaliza a dongosolo la kachitidwe ka zinthu la Satana, chomwe chimatanthauza kuti “kamtsalira kanthaŵi” iye ndi machenjera ake asanaimitsidwe. Makonzedwe kaamba ka mpumulo kuchokera ku chisonkhezero cha usatana chimenechi alongosoledwa mophiphiritsira ndi Yohane mtumwi wa Yesu: “Ndipo ndinawona mngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chifungulo cha phompho, ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthaŵi.”—Chibvumbulutso 12:12; 20:1-3.

Kuchotsa Thayo la Zida Zankhondo

Pamene mazikowo achotsedwa, chisonkhezero chake chonse choipa chidzatha. Kuti atheketse nyengo ya zaka chikwi imeneyi ya mtendere wobwezeretsedwa pa dziko lapansi, Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse iyemwini, adzachotsa thayo lotsendereza la zida zankhondo: “Idzani, penyani ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi. Aletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.”—Salmo 46:8, 9.

Mamiliyoni a anthu akudzikonzekeretsa kale iwo eni kukhala pansi pa mikhalidwe ya mtendere yoteroyo. Mboni za Yehova zikukwaniritsa kale ulosi uwu: “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Chotero, iwo satenga mbali mu mtundu uliwonse wa malonda a zida zankhondo. Mofanana ndi Yesu ndi ophunzira ake, iwo amasungirira kaimidwe kauchete pa nkhani za ndale zadziko ndipo samatengamo mbali mu nkhondo kapena kuwombana kwakudziko, mosasamala kanthu za chirichonse.—Yohane 17:16.

Mogwirizana ndi ulosi wokwaniritsidwa wa Baibulo, nthaŵi yayandikira pamene chida sichidzasulidwira nkhondo, pamene magwero onse a dziko lapansi adzagwiritsiridwa ntchito kokha kaamba ka ubwino wa nzika zake. Kalonga wa Mtendere, Yesu Kristu, Mfumu ya dziko lonse lapansi, akutsimikizira ichi: “Pakuti adzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi, nadzapulumutsa moyo wa aumphaŵi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wawo udzakhala wa mtengo pamaso pake.” Chotero, sangalalani! Dziko lopanda zida posachedwapa lidzakhala lenileni!—Salmo 72:12-14.

[Zithunzi patsamba 10]

Nthaŵi ikuyandikira pamene sipadzakhalanso nkhondo. M’malomwake, dziko lapansi lidzakhala paradaiso wamtendere

[Mawu a Chithunzi]

U.S. Marine Corps photo

Tahiti Tourist Promotion Board

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena