Anasangalala Kum’maŵa kwa Yuropu
CHILIMWE chathachi anthu zikwi makumi ambiri anapita muunyinji wawo kumizinda yaikulu Kum’maŵa kwa Yuropu. Makwalala a Budapest wokongola, Prague, Zagreb, ndi mizinda ina yoposa 20 anadzala anthu ovala mabaji amawonekedwe obiriŵira ndi oyera. Ameneŵa anaŵadziŵikitsa monga okonda ufulu waumulungu ofika pamisonkhano ya Mboni za Yehova.
Kwanthaŵi yoyamba chikhalire, misonkhano inachitika momasuka m’malipabuliki a ku Yuropu a Soviet Union, pamodzi ndi ku Siberia wakutali ndi lipabuliki la ku Asia la Soviet Union lotchedwa Kazakhstan. Onse pamodzi, osonkhana oposa 370,000 anasangalala ndi unansi wabwino ku Chekosolovakiya, Hungary, Yugoslavia, Poland, Romania, ndi Soviet Union.
Kungakhale kovuta kwa amene sanalipo kuyerekezera chisangalalocho pamene oposa 74,252 anasonkhana ku Soviet Union kulambira Yehova Mulungu poyera ndi mopanda mantha. Komabe, chimwemwe chawo chachikulucho sichikanaposa cha okwanira 74,587 m’Prague ndi 40,601 m’Budapest amene anasonkhana m’mabwalo aakulu koposa amaseŵera ku Chekosolovakiya ndi Hungary, kapena cha okwanira 14,684 amene anasonkhana m’Zagreb, Yugoslavia.
Zimenezi nzodabwitsa kwambiri chifukwa chakuti kwazaka zingapo zokha zapitazo, Mboni za Yehova zinali zoletsedwa m’maiko ochuluka a Kum’maŵa kwa Yuropu. Zinali zolekanitsidwa ndi maiko a Kumadzulo mkati mwa Nkhondo Yoputana ndi Mawu. Ngakhale kusonkhana m’timagulu tating’ono kulambira Mulungu kunali kosaloleka. Nkosadabwitsa kuti panali chisangalalo choterocho pokhala okhoza kusonkhana momasuka pamisonkhano yaikulu!
Mboni ya ku Chekosolovakiya yazaka 59, imene inabindikiritsidwa yokha kwamiyezi isanu ndi itatu pafupifupi zaka 40 zapitazo chifukwa cha chikhulupiriro chake mwa Mulungu, inati: “Ambirife amene tinkakhala m’Prague tinalakalaka kukhala ndi msonkhano waukulu womwe ukalinganizidwa kuchitidwira m’bwalo lino lamaseŵera, koma sitinakhulupirire konse kuti cholakalakachi chikachitikadi mwa njira yozizwitsa motere.”
Milungu iŵiri msonkhano usanayambe ku Prague, kuyambira August 9 mpaka 11, nyuzipepala ya mzindawo, Večerník Praha, inati: “Chifukwa chopezedwa ndi mlandu waukulu wakuukira boma ndi kutsutsa chisosholizimu, Mboni za Yehova zinaponyedwa m’ndende Zachikomyunisiti kwazaka zambiri.” Italongosola kuti mzindawo posachedwa ukalandira zikwi makumi ambirimbiri za Mboni, nkhaniyo inamaliza kuti: “Mwachiwonekere simudzakumanapo ndi anthu ochuluka osiyanasiyana ndi omamwetulira m’Prague panthaŵi ina iriyonse kusiyapo mkati mwa kothera kwa mlungu wachiŵiri wa August.”
Komabe, inu mungafunse kuti: ‘Kodi Mboni za Yehova zinazunzidwapo pachifukwa chomveka? Kodi zinakhalapo chiwopsezo ku maulamuliro andale a maiko amene zinakhala? Kodi nthumwi za msonkhano zikwi mazana ambirimbiri Kum’maŵa kwa Yuropu zinachokera kuti? Pokhala zotsenderezedwa ndi zolekanitsidwa ku maiko a Kumadzulo kwazaka 40 kapena kuposapo, kodi zinali zokhoza motani kuchuluka kufikira ziŵerengero zoterozo?’