Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 6/8 tsamba 3-4
  • Kodi Ndani Afuna Kukhala Mponda Matiki?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Afuna Kukhala Mponda Matiki?
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Malotale Kodi Nchifukwa Ninji Ali Otchuka?
    Galamukani!—1991
  • Malotale—Kodi Ndani Amapambana? Kodi Ndani Amalephera?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Kutchova Juga Kulidi Koipa Kwambiri?
    Galamukani!—1991
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 6/8 tsamba 3-4

Kodi Ndani Afuna Kukhala Mponda Matiki?

MWACHIWONEKERE yankho liyenera kukhala lakuti: pafupifupi aliyense. Ndipo njira yosavutiratu yokhalira wotero—malinga ndi malingaliro ofala—ndiyo kupeza ndalama zochuluka mwamsanga m’malotale kapena kubetcha m’maseŵera a mpira wachitanyu.a

Mwakutsatira mzimu umene wafala—ndi kufuna ndalama zowonjezereka zomwe malotale amadzetsa—maboma ambiri kuyambira ku Moscow mpaka Madrid, Manila mpaka Mexico City, amachirikiza malotale Aboma omwe amapereka mphotho ya ndalama zomwe zimafika ku madola mamiliyoni zana limodzi.

Anthu oŵerengeka amakhaladi amponda matiki. Mngelezi wina anadzaza matikiti obetchera m’maseŵera ampira wachitanyu kwa zaka 25 asanapeze mphotho ya ndalama zochuluka koposa. Mwakubetcha masenti 50, anapambana pafupifupi $1.5 miliyoni. Yodabwitsa kwambiri inali mphotho yopatsidwa kwa mkazi wina wa ku New York, yemwe anakhala mmodzi wa opambana koposa padziko pamene anapata $55 miliyoni m’lotale ya Boma ku Florida.

Koma zimenezo nzakamodzikamodzi. Chitsanzo cha zochitika zakaŵirikaŵiri ndicho nkhani yonena za kalaliki Wachispanya wazaka zapakati yemwe anagula matikiti a lotale mlungu uliwonse kwa zaka 30. Ngakhale kuti sanapambanepo mphotho yeniyeni, akupitirizabe kumabetcha. “Nthaŵi zonse ndimawona kuti ndidzapambana,” iye akutero. Mofananamo, mwamuna wina ku Montreal, amene anathera malipiro amlungu wathunthu m’lotale ya ku Canada, anasonyeza lingaliro la ambiri pamene anati: “Kubetcha koteroko ndiko njira yokha yowoneka kukhala yotheka kwa anthu wamba yopezera moyo wabwinopo.” Koma nayenso sanapambanepo.

Mosasamala kanthu za chisonkhezero chofala cha malotale, pali mtundu wina wa kutchova juga umene ukutchuka kwambiri: kuseŵera makina otchovera juga otchedwa slot machine. Ngakhale kuti makinawa, amene tidzawatcha achifwamba adzanja limodzi, samapereka chuma mwamsanga, amapatsadi wowaseŵera mwaŵi wakupambana jakipoti panthaŵi yomweyo—umene ukhoza kuchitikadi. Ndipo sakupezeka m’nyumba zotchovera juga zokha. Nyimbo zokopa za makinawo, magetsi ake ong’anima, ndi kulira kwa makobiri oponyedwamo zimakopa anthu m’makefi a ku Yuropu, makalabu, nyumba zodyera, ndi mahotela.

Frances ndimkazi wamasiye yemwe amakhala mu New York City. Kaŵiri mwina katatu mlungu uliwonse, amatenga ulendo wamaola aŵiri ndi theka pabasi kupita ku Atlantic City, New Jersey. Atafika kumeneko amaloŵa m’nyumba ina yotchovera juga mumzindawo, ndipo m’menemo amaseŵera makina otchovera juga kwa maola asanu ndi limodzi kapena oposapo asanabwerere kunyumba. “Sindidziŵa chomwe ndingachite popanda Atlantic City,” akutero mkaziyo. “Aŵatu ndiwo maseŵera athu omwe timachita.”

Ena amatchova juga kaamba ka zifuno zina pambali pakusanguluka. Imakhalanso, njira yopezera mpumulo ku zochita za moyo watsiku ndi tsiku, kapena kuyesayesa kupeza chuma. Kwa iwo kuli kofunika—ngati sindiko chinthu chachikulu—m’moyo.

“Ndine wotchova juga chifukwa chakuti upandu woloŵetsedwamo umandisangalatsa,” akufotokoza motero Luciano, wa ku Córdoba, Spanya. “Sindikunena modzichinjiriza,” akuwonjezera motero, “koma chenicheni nchakuti ndinachita tondovi, ndicho chifukwa chake ndinayamba kuseŵera juga ya bingo. Ndiyeno ndinafunafuna maseŵera ena amwaŵi. Umadziwona kukhala kanthu ngati uli ndi ndalama m’thumba ndi wokonzekera kuseŵera.” Wotchova juga wina wanthaŵi zonse, yemwe anataya ntchito yake yoyang’anira kampani, anafunsidwa ngati analingalirapo za kusiya chizoloŵezi chake. “Munena za kusiya?” anayankha motero. “Kutalitali, sindingachite zimenezo. Ndiwo umoyo wanga umenewu.”

Ngakhale kuti zolinga zingasiyane, otchova juga saali gulu laling’ono konse. Pamlingo wokulira kapena wochepa, achikulire Achimereka 3 mwa 4 amatchova juga; chiŵerengero cha ku Spanya, dziko lina kumene kutchova juga kuli kofala, nchofanana. Ndipo kutchova juga kuli malonda aakulu. Kokha zigwirizano zochepa za maindasitale padziko lonse ndizo zimachita malonda omwe amadzetsa ndalama zoposa zija zopezedwa m’malotale m’maiko 39 kuwaika pamodzi.

Mowonekeratu, chinyengo cha kutchova juga nchamphamvu. Koma kodi chiridi chosangulutsa chosavulaza, kapena kodi chiri ndi maupandu obisika? Mwambi wamakedzana umachenjeza kuti: “Wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.” (Miyambo 28:20) Kodi zimenezi ziridi tero kwa amene angalemere mwakutchova juga?

[Mawu a M’munsi]

a Kubetcherana zotulukapo za maseŵera a mpira wachitanyu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena