Mwana Wanu Ali Paupandu!
Kugona ana kuli chochitika chowopsa m’dziko lino loipa. Magazini otchedwa Lear’s anati: “Kumayambukira ambiri a ife kuposa kansa, ambiri a ife kuposa nthenda ya mtima, ambiri a ife kuposa AIDS.” Chotero atolankhani a Galamukani! akuona kukhala thayo lawo kudziŵitsa oŵerenga awo za ngozi imeneyi ndi zimene zingachitidwe.—Yerekezerani ndi Ezekieli 3:17-21; Aroma 13:11-13.
M’ZAKA zaposachedwapa mkwiyo wotsutsa kugona ana wasonyezedwa padziko lonse. Koma nkhani zofalitsidwa, zosimba za anthu ambiri otchuka amene anena poyera kuti anagonedwapo paubwana, zachititsa malingaliro olakwika kukhalako. Ena amakhulupirira kuti nkhani zonsezi za nkhanza pa ana zangokhala chizoloŵezi chatsopano chofala chapakanthaŵi. Koma kunena zowona, palibe chatsopano kwenikweni ponena za nkhanza yogona ana imeneyo. Iko kwakhalako pafupifupi kwa utali umene mbiri ya anthu yakhalapo.
Vuto Lamakedzana
Pafupifupi zaka 4,000 zapitazo, mizinda ya Sodomu ndi Gomora inali yotchuka ndi khalidwe loluluzika. Mwachionekere kugona ana kunali pakati pa zonyansa zambiri zochitidwa m’deralo. Lemba la Genesis 19:4 limafotokoza gulu la anthu a m’Sodomu lolakalaka kugonana “anyamata ndi okalamba” lofuna kugwirira chigololo alendo aŵiri aamuna a Loti. Talingalirani: Nchifukwa ninji anyamata wamba anatenthedwa mtima ndi lingaliro la kugwirira chigololo amuna? Mosakayikira iwo anali ataphunzitsidwa kale machitachita oluluzika a kugonana kwa amuna okhaokha.
Zaka mazana ambiri pambuyo pake, mtundu wa Israyeli unaloŵa m’dera la Kanani. Dzikoli linali lomwerekera kwambiri m’kugonana kwa pachibale, kugonana kwa ofanana ziŵalo, kugonana ndi zinyama, uhule, ndipo ngakhale madzoma akupereka nsembe za makanda kwa milungu yauchiŵanda kotero kuti machitidwe onyansa ameneŵa analetsedwa mosabisa m’Chilamulo cha Mose. (Levitiko 18:6, 21-23; 19:29; Yeremiya 32:35) Mosasamala kanthu za machenjezo aumulungu, Aisrayeli opanduka, kuphatikizapo ena a olamulira awo, anatengera machitachita oipa ameneŵa.—Salmo 106:35-38.
Komabe, Girisi ndi Roma wamakedzana anali oipitsitsa m’zimenezi kuposa Israyeli. Kupha ana kunali kofala m’maiko aŵiriwo, ndipo m’Girisi kugonana kwa amuna achikulire ndi anyamata achichepere kunali mchitidwe wovomerezeka kwambiri. Nyumba za mahule achinyamata zinali zofala mumzinda uliwonse wamakedzana m’Girisi. Mu ufumu wa Roma, uhule wa ana unali wofala kwambiri moti misonkho ndi maholide apadera anakhazikitsidwa kaamba ka malondawo. M’mabwalo amaseŵera, atsikana anali kugwiriridwa chigololo ndi kukakamizidwa kugonana ndi zinyama. Nkhanza zofanana zinali zofala m’maiko ena amakedzana.
Bwanji m’nthaŵi zamakono? Kodi anthu ngopita patsogolo kwambiri kotero kuti machitidwe akugonana otero ochititsa kakasi sangafalikire lerolino? Ophunzira Baibulo sangavomereze lingaliro limeneli. Amadziŵa bwino lomwe kuti mtumwi Paulo anatcha nyengo yathu kukhala “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Iye anafotokoza mwatsatanetsatane kudzikonda kofala, kukonda zokondweretsa, ndi kunyonyotsoka kwa chikondi m’banja kumene kwakantha chitaganya chamakono nawonjezera kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire.” (2 Timoteo 3:1-5, 13; Chivumbulutso 12:7-12) Kodi kugona ana, kochitidwa kaŵirikaŵiri ndi “anthu oipa ndi onyenga,” kwaipa chiipire?
Vuto Lofuna Kuchitapo Kanthu Msanga
Kaŵirikaŵiri nkhanza pa ana zimachitidwa m’seri, moti zafikira pakunenedwa kukhala maupandu osachitiridwa lipoti kwa apolisi. Ngakhale nditero, maupandu otero mwachionekere awonjezereka m’zaka makumi angapo zaposachedwapa. Ku United States, kufufuza nkhaniyo kunachitidwa ndi Los Angeles Times. Inapeza kuti 27 peresenti ya akazi ndi 16 peresenti ya amuna anachitiridwa nkhanza ya kugonedwa akali ana. Ngakhale kuti ziŵerengero zimenezi nzodabwitsa, ziŵerengero zina zopezedwa mosamalitsa za United States zakhala zochuluka koposerapo.
Ku Malaysia, malipoti a kugonedwa kwa ana awonjezereka kuŵirikiza kanayi m’zaka khumi zapitazo. Ku Thailand, pafupifupi 75 peresenti ya amuna m’kufufuza kwina anavomereza kuti anagonana ndi ana amene ndimahule. Ku Germany, akuluakulu a boma akuyerekezera kuti ana pafupifupi 300,000 amagonedwa chaka chilichonse. Malinga nkunena kwa Cape Times ya ku South Africa, chiŵerengero cha malipoti a nkhanza zotero chinawonjezeka ndi 175 peresenti m’nyengo ya zaka zitatu yaposachedwapa. Ku Netherlands ndi Canada, ofufuza anapeza kuti mkazi mmodzi mwa atatu aliwonse anagonedwapo akali mwana. Ku Finland, 18 peresenti ya atsikana a m’giredi lachisanu ndi chinayi (a zaka 15 kapena 16) ndi 7 peresenti ya anyamata anasimba kuti anagonanapo ndi wina amene anali wamkulu kwa iwo ndi zaka zosachepera pa zisanu.
M’maiko ambiri malipoti osautsa avumbuluka onena za timagulu tachipembedzo timene timachitira nkhanza ana ndi machitachita akuwagona mwauchinyama ndi kuwazunza. Kaŵirikaŵiri, awo amene amanena kuti anachitiridwa maupandu otero samakhulupiriridwa, ndipo samachitiridwa chifundo.
Chotero kugona ana sikuli kwatsopano ndipo nkofala; ndivuto limene lakhalako kwa nthaŵi yaitali limene lakhala lowanda kwambiri lerolino. Chiyambukiro chake chingakhale chosakaza. Ambiri amene anagonedwapo amazunzika ndi malingaliro osautsa a kukhala wopanda pake ndi wonyozeka. Akatswiri pankhaniyi andandalika ziyambukiro zina zofala za kugonedwa ndi achibale kwa atsikana, zonga ngati kuthaŵa panyumba, kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi uchidakwa, kuchita tondovi, kuyesa kudzipha, kupulupudza, uchiwerewere, kulephera kugona tulo tabwino, ndi vuto la kusakhoza kuphunzira. Ziyambukiro zokhalitsa zingaphatikizepo kusoŵa maluso aukholo, kusoŵa chilakolako cha kugonana, kusakhulupirira amuna, kukwatiwa kwa wokonda kugonana ndi ana, kugonana ndi akazi anzawo, uhule, ndi kugona ana kwenikweniko.
Sikuti ziyambukiro zimenezi zili zosapeŵeka kwa wogonedwapoyo; ndipo aliyense sangalekerere mkhalidwe woipa kokha chifukwa chakuti anachitiridwa nkhanzayo kalelo. Nkhanza yakugonedwa simachititsa kuti wogonedwapoyo adzakhale wachisembwere kapena wopulupudza; ndipo simafafaniza thayo lawo lonse pa zosankha zimene amapanga m’moyo pambuyo pake. Koma zotulukapo zofala zimenezi za ogonedwapo paubwana nzowopsa kwambiri. Zimachititsa funso lotsatira kukhala lofunika kwambiri, Kodi tingatetezere motani ana kunkhanza ya kugonedwa?