Minkhole Yopanda Liŵongo ya Kuchitira Nkhanza Ana
“NDIKUYANDIKIRA zaka 40 zakubadwa tsopano,” akutero Eilene.a “Ndipo ngakhale kuti vuto langa lakhala koposa zaka 30, likundisautsabe. Chifukwa cha vuto langa, ndimakhala wokwiya, kudzimva waliŵongo, ndipo ndiri ndi mavuto muukwati wanga! Anthu amayesa kumvetsetsa chisoni changa, koma sangathe.” Kodi Eilene ali ndivuto lanji? Iye ali mnkhole wa nkhanza ya kugonedwa paubwana, ndipo kwa iye ziyambukirozo zatsimikizira kukhala zokhalitsa.
Ndithudi, Eilene sali yekha m’nkhaniyi. Kufufuza kumasonyeza kuti chiŵerengero chochititsa mantha cha akazi—ndi amuna—avutika ndi kuchitiridwa moipa koteroko.b Popeza kuti nkhanza yakugona ana siiri konse mchitidwe wakamodzikamodzi woipa, iyo iri vuto lofalikira kwambiri, limene limapezeka m’magulu onse a anthu a mayanjano, a zachuma, a chipembedzo, ndi a mafuko.
Mwamwaŵi, amuna ndi akazi ambiri sakalingalira konse za kuchitira mwana mwanjira yoipa imeneyi. Koma ochepa oipitsitsa ali ndi chikhoterero choipa chimenechi. Ndipo mosiyana ndi omwerekera m’khalidwe woterowo, ochitira nkhanza ana oŵerengeka ali anthu odwala maganizo okhala ndi zizoloŵezi zakupha ndipo amabisala m’mabwalo oseŵerera. Ambiri ali anthu amene kunja amakhala ndi mawonekedwe abwino okhutiritsa. Iwo amakhutiritsa zilakolako zawo zoipa mwakulungama ana osadziŵa kanthu, owadalira, osatha kudzichinjiriza—kaŵirikaŵiri ana awo aakazi enieniwo.c Poyera, amachitira anawo mokoma mtima, mwachikondi. Mtseri, amawaloŵetsa m’kugonana kowopseza, kwachiwawa, ndi kwamanyazi.
Zowonadi, nkovuta kumvetsetsa kuti zowopsa zoterozo zingakhale zikuchitika m’nyumba zambiri zowoneka kukhala zolemekezeka. Komabe, ngakhale m’nthaŵi za Baibulo, ana anagwiritsiridwa ntchito “kaamba ka chikhutiritso cha panthaŵiyo cha . . . chilakolako chakugonana.” (The International Critical Commentary; yerekezerani ndi Yoweli 3:3.) Baibulo linalosera kuti: ‘Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha . . . opanda chikondi chachibadwidwe . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.’ Chotero, siziyenera kutidabwitsa kuti nkhanza pa ana ikuchitika pamlingo waukulu lerolino.—2 Timoteo 3:1, 3, 13.
Kuchitiridwa zoipa paubwana sikungasiye zipsera zakuthupi. Ndipo siakulu onse omwe anapangidwa minkhole paubwana wawo amene akuwoneka kukhala ovutitsidwa nazo. Koma monga momwe mwambi wakale unanenera: “Ngakhale m’kuseka mtima uwawa.” (Miyambo 14:13) Inde, minkhole yambiri iri ndi zipsera zakuya za malingaliro—mabala obisika amene akutukusira mkati. Komabe, kodi nchifukwa ninji kuchitira ana zoipa kumachititsa chivulazo choterocho? Kodi nchifukwa ninji mabalawo samapola okha m’kupita kwanthaŵi? Kukula kwa vuto losautsa limeneli kumafunikiritsa kuti tisumikepo maganizo athu. Nzowona, zina zimene zikutsatirapo zingakhale zosakondweretsa kuziŵerenga—makamaka ngati munali mnkhole wa kuchitiridwa nkhanza paubwana. Koma khalani wotsimikiziridwa kuti chiyembekezo chiripo, mukhozadi kuchira.
[Mawu a M’munsi]
a Maina onse asinthidwa.
b Chifukwa chakuti mamasuliridwe a nkhanza yakugonana ndi njira zofufuzira zimasiyana mokulira, maŵerengedwe olongosoka ali pafupifupi osatheka kuwapanga.
c Minkhole yambiri imachitidwa choipa ndi atate awo enieni kapena atate opeza. Ochitira zoipa angakhalenso akulu awo, amalume, agogo aamuna, odziŵana nawo achikulire, ndi alendo. Popeza kuti minkhole yambiri ndi akazi, kwakukulukulu tidzalozera kwa iwo. Komabe, chidziŵitso choperekedwa pano chimagwira ntchito kwa onse.