Kutonthoza Achikulire Amene Anapyola Kusweka Mtima Kwapaubwana
IWO anali okwatirana achichepere okonda mayanjano, olemekezeka kwambiri mumpingo. Koma mawu a mwamuna anali ochonderera pamene anapempha ngati mkulu angawachezere, ndipo mkazi wake anali kugwetsa misozi. Mkaziyo anali kuvutika ndi nyengo za kuchita tondovi kowopsa ndi kudzida, ngakhale malingaliro a kudzipha. Iye anagonedwapo pamene anali wachichepere. Ali wokondwa kuti gulu la Yehova lapereka malangizo othandizira mikhole ya upandu wotero, mkuluyo anaŵerenga makalata amene Sosaite inalembera akulu limodzinso ndi nkhani za mu Galamukani! wa October 8, 1991, ndi nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1984 imene inafotokoza za nkhani imeneyi. Nazi mfundo zingapo zothandiza zotengedwa m’magwero ameneŵa.
1. Mvetserani, mvetserani, mvetserani. Pamene mwana adzimyula pabondo, lingaliro lake loyambirira nlakuthamangira kwa Amayi kapena Atate kuti akamtonthoze. Koma mwana wogonedwa mwina angakhale alibiretu lingaliro limenelo. Chotero monga wachikulire, iye amakhalabe ndi chikhumbo chimodzimodzicho—cha kuulula, kukambitsirana nkhaniyo, kutonthozedwa ndi womvetsera wachifundo. (Yerekezerani ndi Yobu 10:1; 32:20.) Pamene mkulu anakachezera okwatirana otchulidwawo, mwamunayo anadabwa kuona mkuluyo akulankhula pang’ono ndi kumvetsera kwambiri. Mwamuna wakeyo, pokhala wothandiza, wofuna kuona kuti zinthu zikuyenda bwino, anapeza kuti anali kuyesa kuthetsa vuto la kupsinjika mtimalo ndi luntha, akumayesa kuwongolera malingaliro amene anaoneka kukhala osayenera kwa iye. Anaphunzira kuti mkazi wake anafunikira kuchitiridwa chifundo kwambiri osati mayankho chabe. (Yerekezerani ndi Aroma 12:15.) Mkaziyo anafuna kumva kuti zifukwa zimene anali nazo zochitira tondovi motero zinali zomveka.
2. Vumbulani mabodza. Kugona ana kumaphunzitsa ana kuti ali odetsedwa, osakondeka, opanda pake. Mofanana ndi ziphunzitso zonama zachipembedzo, malingaliro ameneŵa angachititse unansi wabwino ndi Yehova kukhala wovuta kwambiri. Chotero vumbulani mabodza, ndipo ikani chowonadi mmalo ake—mofatsa, mobwerezabwereza, moleza mtima. Kambitsiranani za m’Malemba. (2 Akorinto 10:4, 5) Mwachitsanzo munganene kuti: “Ndikudziŵa kuti mukudzimva kukhala wodetsedwa. Koma kodi Yehova amakuonani motani? Ngati analola Mwana wake kufa ndi kupereka dipo kaamba ka inu, kodi zimenezo sizimatanthauza kuti amakukondani? [Yohane 3:16] Kodi kugonedwa kwanu kunakuchititsani inu kukhala wodetsedwa pamaso Pake, kapena kodi kunachititsa wokugonani kukhala wodetsedwa? Kumbukirani kuti Yesu anati: ‘Kulibe kanthu kamene kachokera kunja kwa munthu kuloŵa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zotuluka mwa munthu ndizo zimamdetsa munthu.’ [Marko 7:15] Kunena zowona, kodi ndinu, monga mwana wamng’ono, amene munayambitsa kugonedwako? Kapena kodi ndiwokugonaniyo amene analinganiza zimenezo m’maganizo ake?”
3. Lankhulani motonthoza. Munthu aliyense ngwosiyana, chotero uphungu wa Paulo wa ‘kulankhula motonthoza kwa miyoyo yopsinjika’ umagwira ntchito mosiyanasiyana pachochitika chilichonse. (1 Atesalonika 5:14, NW ) Komabe, kukambitsirana mopeputsa nkhaniyo sikumatonthoza kwambiri. Mwachitsanzo, kungouza amene anagonedwapo kuŵerenga Baibulo kwambiri, kulalikira kwambiri, kapena ‘kungosenzetsa Yehova nkhaŵa yake’—ngakhale kuti malingaliro ameneŵa ali othandiza nthaŵi zina—mwina sikungakhale ndi zotulukapo zabwino. (Salmo 55:22; yerekezerani ndi Agalatiya 6:2.) Ambiri akuyesayesa malinga nkukhoza kwawo kuchita zinthu zimenezi mwanjira yabwinopo ndipo amadziimba mlandu wa kusachita bwino koposa.—Yerekezerani ndi 1 Yohane 3:19, 20.
Mofananamo, kuuza amene anagonedwapo kungoiŵala zakale kungaipitsirepo mkhalidwewo mmalo mouwongolera. Akanakhoza kutero, mosakayikira akanatero—ndipo sakanafunikira chithandizo kuti apeze njira yosavutayo yothetsera vuto lawo.a Kumbukirani, kusweka mtima kwawo nkwakukulu. Tingoyerekezera chabe, talingalirani kuti mwapeza munthu amene wapezeka m’ngozi ya galimoto aligone pakati pa zitsulo akubuula. Kodi mudzangomuuza kusalingalira za ululu? Mwachionekere pafunikira kuchitapo kanthu.
Ngati simuli wotsimikiza kuti zimene mukunena zili zotonthoza ndi zothandiza, bwanji osamfunsa wochita tondoviyo? Ndi iko komwe, ngakhale uphungu umene uli wowona ndi wa m’Malemba uyenera kukhala wapanthaŵi yake ndiponso woyenerera.—Yerekezerani ndi Miyambo 25:11.
Pambuyo pamaulendo ocheza angapo, mlongoyo anayamba kuona kuongokera kwa kaonedwe kake ka zinthu, ndipo mwamuna wake anakhoza bwino lomwe kumthandiza kupyola m’nthaŵi zovutazo. Kuyambira nthaŵiyo onse aŵiri akhoza kulankhula motonthoza kwa ena amene apyola kusweka mtima kofananako. Nkolimbitsa chikhulupiriro chotani nanga kuona Yehova, “Mulungu wa chitonthozo chonse,” akugwira ntchito kupyolera m’Mawu ake ndi anthu ake ‘kumanga osweka mtima’ m’nthaŵi zino zoŵaŵitsa.—2 Akorinto 1:3; Yesaya 61:1.
[Mawu a M’munsi]
a Zowona, mtumwi Paulo analangizadi Akristu ‘kuiŵala zam’mbuyo.’ Koma Paulo panopo anali kunena za ulemerero wake wakale ndi chipambano cha kudziko, zimene tsopano zinali “zapadzala” kwa iye. Sanali kunena za masautso ake akale, amene anasimba mwaufulu.—Afilipi 3:4-6, 8, 13; yerekezerani ndi 2 Akorinto 11:23-27.