Gulu Lotchuka la Nyengo Yatsopano
TIKUKHALA m’nyengo yovuta kwambiri. Miyambo ndi njira za moyo zikukayikiridwa mosalekeza. Msanganizo wowopsa wa chipembedzo ndi ndale ukutikankha kuchoka ku tsoka limodzi kumka ku linzake. Sayansi ndi luso la zopangapanga sizinabweretse mayankho okhalitsa a mavuto a anthu. Ambiri ngotsimikizira kuti mkhalidwe wa zinthu woterowo sungathetsedwe kusiyapo kokha ngati kutabwera dongosolo la dziko latsopano kotheratu.
Koma kodi nyengo imeneyo idzabwera motani? Mwa kuloŵererapo kwa Mulungu? Ngati ndichoncho, kodi tiyenera kupitiriza kudikira? Kapena kodi tingachitepo kanthu ife enife? Kodi tingadzetse nyengo yatsopano yofunidwa kwambiriyo? Anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse a m’mikhalidwe yonse ya moyo amakhulupirira kuti angachite mbali yokangalika kubweretsa nyengo yatsopano ya mtendere ndi ubale. Iwo ali mbali ya gulu losintha zinthu la Nyengo Yatsopano, ndipo akufuna kuti mugwirizane nawo!
Gulu Lapadziko Lonse
Kodi munayamba mwamvapo za gulu la Nyengo Yatsopano? M’maiko ambiri liwu lakuti “Nyengo Yatsopano” lagwiritsidwa ntchito mofala pamitundu ina yotchuka ya mabuku, nyimbo, ndi maluso ena. Modabwitsa, pali ngakhale malesitilanti a Nyengo Yatsopano! Akatswiri a zamaseŵera ndi ngwazi za ku Hollywood amachirikiza gululo. Mamembala ake amachita misonkhano ndi zionetsero nthaŵi zonse. Liwu lakuti “Nyengo Yatsopano” lagwirizanitsidwanso mofala ndi zinthu zogwiritsira ntchito, monga ngati zodzoladzola, zinthu zokongoletsera thupi, mavitamini, ndi zinthu zina zaukhondo. Mabuku onena za Nyengo Yatsopano amagulitsidwa m’mamiliyoni ambiri. Masitolo ena ali ndi chigawo chapadera cha mabukuwo. Ambiri a mabuku ameneŵa ali ndi chisonkhezero champhamvu chachipembedzo pa oŵerenga.
M’buku lake lakuti The Cosmic Self—A Penetrating Look at Today’s New Age Movements, mlembi Ted Peters akutchula za gululo kukhala “lofanana ndi kuphulika kwa bomba [la hydrogen] lachipembedzo kwa nyengo yaitali ya zaka pafupifupi makumi atatu tsopano.” Iye akuwonjezera kuti “aneneri a gulu la nyengo yatsopano akupanga ophunzira; ndipo ziphunzitso zawo zikulandiridwa . . . ndi Aprotesitanti, Aroma Katolika, Ayuda, osakhulupirira kukhalapo kwa Mulungu, limodzinso ndi chiŵerengero chomawonjezereka cha Abuddha ndi Ahindu ku North America.”
The Times ya ku London ikusimba kuti “Chikhulupiriro cha Nyengo Yatsopano . . . mwinamwake tsopano chili chofalikira mofulumira kwambiri Kumadzulo. Kwayerekezeredwa kuti, posachedwapa, chiŵerengero cha anthu a ku America 25 peresenti adzalandira kumlingo wina wake Chikhulupiriro cha Nyengo Yatsopano.” Magazini a ku Switzerland a Fundamentum ananena kuti, ku Netherlands, akatswiri azaumulungu pafupifupi zana limodzi anali kusonkhana mokhazikika “kuti akambitsirane mmene kulingalira kwa Nyengo Yatsopano kungayambitsidwire m’moyo wa tchalitchi ndiponso m’maulaliki.” Magazini ena akulengeza kuti “maiko padziko lonse ali ndi njira zawo zosiyanasiyana za Nyengo Yatsopano, koma chikoka chake chili cha padziko lonse.”
Mabungwe a mabizinesi awononga madola mamiliyoni pa aphungu a Nyengo Yatsopano ndi kulembetsa antchito awo m’maprogramu amaphunziro a Nyengo Yatsopano. San Francisco Chronicle ikusimba kuti “kulingalira kwa Nyengo Yatsopano kwaloŵerera m’magulu amphamvu apamwamba koposa a mabizinesi a ku America.” Nyuzipepalayo ikuwonjezera kuti kupendedwa kumodzi kwa makampani 500 kunavumbula kuti oposa 50 peresenti anali oloŵetsedwamo kwambiri ndi kulingalira kwa Nyengo Yatsopano.
Koma kodi chikhoterero cha Nyengo Yatsopano nchiyani, ndipo kodi chinayamba motani? Kodi chidzabweretsadi mtendere ndi chigwirizano pa dziko lapansi? Kodi chimaphunzitsanji, ndipo kodi chimakuyambukirani motani?