Zaka Zoposa 40 Pansi pa Chiletso cha Komyunizimu
YOSIMBIDWA NDI JARMILA HÁLOVÁ
Nthaŵi: pakati pa usiku patapita, February 4, 1952. Malo: m’nyumba yathu ku Prague, Czechoslovakia. Tinadzutsidwa ndi kulira kopitiriza kwa belu lapakhomo. Ndiyeno apolisi analoŵa m’nyumba.
APOLISI anaika Amayi, Atate, mlongo wanga Pavel, ndi ineyo m’zipinda zosiyanasiyana, anatiikira mlonda aliyense wa ife, nayamba kufunafuna m’zinthu zonse. Iwo anali kufufuzabe m’nyumbamo pafupifupi maola 12 pambuyo pake. Atapenda mabuku onse amene anapeza, anawaika m’mabokosi.
Pambuyo pake, anandilamula kuloŵa m’galimoto, ndipo anandiveka magalasi akuda. Zimenezo zinaoneka zachilendo, koma ndinakhoza kusendeza pang’ono magalasiwo kuti ndione kumene anali kundipereka. Misewu yake inali yodziŵika. Tinali kupita kumalikulu a mbiri yoipa a State Security.
Anandikankhira kunja kwa galimoto. Pambuyo pake pamene anandivula magalasi, ndinali m’kachipinda kena kauve. Mkazi wina wovala yunifomu anandilamula kuvula zovala ndi kuvala thalauza yolimba ya ntchito ndi malaya achimuna. Anandimanga kansalu kumutu kuphimba maso anga, ndipo ananditulutsa m’chipindacho, ndili womanga kumaso, nayenda nane m’malikole ochita ngati osatha.
Potsiriza, mlondayo anaima natsegula chitseko chachitsulo, ndipo anandikankhira mkati. Anakang’amba kansaluko kumutu kwanga, nanditsekera. Ndinali m’lumande ya ndende. Munali mkazi wina wazaka za m’ma 40 amene anali kundipenya, atavala zovala zonga zanga. Zimenezo zinandikondweretsa ndipo—ngakhale kuti zingaoneke zachilendo—sindinachitire mwina koma kuseka. Pokhala msungwana wazaka 19, amene anali wosadziŵa chinthu chonga kuponyedwa m’ndende, mtima sunagunde. Posapita nthaŵi, ndinakondwa kwambiri kudziŵa kuti panalibe wina aliyense wa m’banja lathu amene anagwidwa.
Kunali kwangozi zaka zimenezo kukhala Mboni ya Yehova m’dziko limene panthaŵiyo linali Czechoslovakia. Dzikolo linali kulamuliridwa ndi Akomyunizimu, ndipo Mboni zinali zoletsedwa. Kodi zinachitika bwanji kuti banja lathu ligwirizane kwambiri ndi gulu loletsedwa?
Mmene Tinakhalira Mboni
Atate, nzika ya Prague, anakulira m’Chiprotesitanti ndipo anali odzipereka kwambiri pa zikhulupiriro zawo. Anakumana ndi Amayi m’ma 1920 pamene iwo anafika ku Prague kudzaphunzira zamankhwala. Iwo anachokera kudera lotchedwa Bessarabia, limene paubwana wawo linali mbali ya Russia. Atakwatirana, iwo anayamba kuloŵa tchalitchi cha atate ngakhale kuti iwo anali Ayuda. Komabe, sichinawakhutiritse.
M’Nkhondo Yadziko II, Atate anaponyedwa mumsasa wachibalo, ndipo Amayi anapulumuka mwamwaŵi m’chipululutsocho. Zaka zimenezo zinali zovuta kwa ife, koma tonsefe tinapulumuka. Chapakati pa 1947, zaka ziŵiri nkhondoyo itatha, mmodzi wa alongo awo a Atate, amene anakhala Mboni ya Yehova, analembetsera banja lathu sabusikripishoni ya Nsanja ya Olonda. Amayi ndiwo anayamba kuiŵerenga, ndipo pomwepo analandira uthengawo monga choonadi chimene anali kufunafuna.
Poyamba, iwo sanatiuze zambiri enafe, koma anapeza kumene misonkhano inali kuchitikira m’Prague nayamba kumapezekako. M’miyezi ingapo, m’ngululu ya 1948, iwo anabatizidwa pamsonkhano wadera wa Mboni. Ndiyeno anatipempha kumapita nawo kumisonkhano. Mwankhokera, Atate anavomera.
Misonkhano inali kuchitikira m’kaholo kena pakati pa Prague, kumene tinayamba kupita monga banja. Ine ndi Atate mitima yathu inali yokayikakayika, inakopeka ndipo inanyumwa. Tinadabwa kuti Amayi anali kale ndi mabwenzi atsopano amene iwo anali kutisonyeza. Ndinachita chidwi ndi chisangalalo chawo ndi kulolera kwawo ena, ndi kuyamikira ubale wawo kumene anasonyeza.
Poona chifuno chathu, Amayi analingalira kuti Mboni ziitanidwe kunyumba kwathu kudzakambitsirana nafe zambiri. Ine ndi Atate tinadabwa kwambiri pamene iwo anatisonyeza m’Baibulo lathu kuti kulibe moyo wosafa ndipo kulibe Utatu! Inde, kunali kotsegula maso kudziŵa zimene kumatanthauzadi kupemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe ndi kuti Ufumu wake udze.
Patapita milungu ingapo, Atate anaitana atsogoleri achipembezo angapo a tchalitchi chawo kunyumba kwathu. Iwo anati: “Abale anga, ndifuna kukambitsirana nanu mfundo zina za m’Malemba.” Atanena zimenezo, anatchula ziphunzitso zoyambirira za tchalitchi mwatsatanetsatane nasonyeza mmene zimenezi zinalili zosiyanira ndi Baibulo. Atsogoleri achipembedzo anavomereza kuti zimene ananena zinali zoona. Ndiyeno Atate anati: “Ine ndasankha kuchoka m’tchalitchi, ndipo ndikukamba moimira banja langa.”
Ntchito Yolalikira Iletsedwa
Mu February 1948, ine ndi Atate titangoyamba kufika pamisonkhano, chipani cha Komyunizimu chinayamba kulamulira dzikoli. Ndinaona ophunzira anzanga akumaneneza aphunzitsi awo, ndipo ndinaona aphunzitsi akuwopa makolo a ophunzira awo. Aliyense anawopa mnzake. Komabe, poyamba, ntchito ya Mboni za Yehova sinakhudzidwe konse.
Kwa ife mbali yapadera mu 1948 inali msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku Prague. Panali anthu oposa 2,800 pa September 10 mpaka 12. Patapita milungu ingapo, pa November 29, 1948, a secret police analanda ofesi ya nthambi, ndipo inatsekedwa. Mu April wa chaka chotsatira ntchito yathu inaletsedwa.
Zochitika zonsezi sizinawopseze banja lathu, ndipo mu September 1949 tinapezeka paprogramu yapadera m’nkhalango kunja kwa Prague. Patapita mlungu umodzi, ine ndi Atate tinabatizidwa. Ngakhale kuti tinayesayesa kukhala osamala m’ntchito yolalikira, ndinagwidwa mu February 1952, monga ndasonyezera poyamba.
Kufunsidwa Mobwerezabwereza
Nditafunsidwa kangapo, ndinalingalira kuti ndidzakhala m’ndendemo nthaŵi yaitali. Ofunsawo anachita ngati anali kuganiza kuti ngati munthu ambindikira kwa nthaŵi yotalikirapo ndipo alibe chochita chilichonse, akafuna kwambiri kupereka thandizo. Koma ndimakumbukirabe malangizo a makolo anga, ndipo anandithandiza kulimbika. Kaŵirikaŵiri iwo anali kugwira mawu Salmo 90:12, akumandilimbikitsa ‘kuŵerenga masiku anga,’ ndiko kuti, kuwapenda, kapena kuwapima, ‘kuti ndikhale nawo mtima wanzeru.’
Chotero, m’maganizo mwanga ndinasinkhasinkha masalmo onse ndi ndime zina za Baibulo zimene ndinaloŵeza pamtima poyamba. Ndinasinkhasinkhanso nkhani za mu Nsanja ya Olonda zimene ndinaphunzira ndisanaponyedwe m’ndende ndipo ndinaimba nyimbo za Ufumu. Ndiponso, m’miyezi yanga yoyamba ya kubindikiridwa, panali akaidi anzanga olankhula nawo. Ndiponso, panali nkhani zina zosinkhasinkha zimene ndinaphunzira m’kalasi kusukulu, pakuti ndinali nditapambana mayeso miyezi ingapo zimenezi zisanachitike.
Kufunsidwako kunandisonyeza kuti munthu wina anafika pa limodzi la maphunziro anga a Baibulo nakandinenera za ntchito yanga ya kulalikira. Akuluakulu a boma anati ndine amenenso ndinatayipa makope a zofalitsa za Baibulo amene anapeza m’nyumba mwathu. Komatu, mlongo wanga, amene anali chabe ndi zaka 15, ndiye anawatayipa.
Patapita nthaŵi, ofunsawo anaona kuti sindidzaulula wina aliyense, choncho anayesayesa kundichotsa pa zikhulupiriro zanga. Ndipotu anandibweretsera munthu wina amene ndinali kumdziŵa kukhala woyang’anira woyendayenda wa Mboni za Yehova. Ngakhale kuti nayenso anali mkaidi, anali kuthandizana tsopano ndi Akomyunizimu pa kuyesa kusonkhezera Mboni zina zomangidwa kukana chikhulupiriro chawo. Anandinyansa chotani nanga! Pambuyo pa zaka, atamasulidwa, uchidakwa wake unamphetsa.
Kubindikiridwa Pandekha
Patapita miyezi isanu ndi iŵiri ndinasamutsidwira ku ndende ina ndi kubindikiridwa pandekha. Tsopano, ndili ndekhandekha, zinali kwa ine kuona mmene ndingagwiritsirire ntchito nthaŵi. Mabuku ankaperekedwa utapempha, koma, monga mudziŵa, osati a zinthu zauzimu. Chotero ndinakonza ndandanda ya zochita yophatikizapo nyengo za kuŵerenga limodzinso ndi nthaŵi ya kusinkhasinkha zinthu zauzimu.
Ndiyenera kunena kuti, ndi kalelonse sindinamvepo kukhala woyandikana kwambiri ndi Yehova m’mapemphero ngati panthaŵiyo. Lingaliro la ubale wathu wa padziko lonse silinakhalepo lamtengo wapatali motero. Tsiku lililonse ndinayesa kuganiza mmene uthenga wabwino unali kufalikira panthaŵi imeneyo kumadera osiyanasiyana a dziko lapansi. Ndinkadziyesa kuti ndikuchitako ntchito imeneyi, kupereka maulaliki a Baibulo kwa anthu.
Komabe, ngakhale m’malo abata ameneŵa, ndinagwidwa mu msampha potsiriza. Popeza kuti nthaŵi zonse ndimakonda kuŵerenga ndipo ndimafuna kudziŵa zimene zinali kuchitika kunja, nthaŵi zina ndimatengeka kwambiri ndi buku lina moti nkunyalanyaza ndandanda yanga ya kusinkhasinkha zinthu zauzimu. Zimenezi zitachitika, ndinkachita chisoni nthaŵi zonse.
Chotero, tsiku lina mmaŵa ndinaperekedwa ku ofesi ya loya. Panalibe zambiri zimene zinakambidwa—kokha zotulukapo za kufunsa kwapapitapo. Ndinalefulidwa, pakuti tsiku la mlandu wanga silinaikidwe. Pafupifupi m’theka la ola, anandibwezera m’lumande mwanga. Mmenemo ndinataya mtima ndi kuyamba kulira. Chifukwa? Kodi kukhala kwanga ndekha kwa milungu yaitali kunali kundigonjetsa tsopano?
Ndinayamba kupenda vuto langa ndipo mwamsanga ndinapeza chochititsa. Tsiku lathalo, ndinatengeka kwambiri ndi kuŵerenga, ndipo sindinadzitangwanitse ndi zochita zanga zauzimu. Chotero pamene ananditenga mwadzidzidzi kukandifunsa, maganizo anga sanali mumkhalidwe wabwino wa pemphero. Pomwepo ndinatsanulira mtima wanga kwa Yehova ndi kulonjeza kuti sindidzanyalanyazanso zinthu zauzimu.
Zimenezo zitachitika, ndinasankhapo kulekeratu kuŵerenga. Ndiyeno nzeru ina yabwino inandifikira, ya kudzikakamiza kuŵerenga Chijeremani. M’Nkhondo Yadziko II, pamene Germany analanda dzikoli, tinakakamizidwa kuphunzira Chijeremani kusukulu. Koma chifukwa cha zinthu zonyansa zimene Ajeremani anali kuchita pamene anali m’Prague, sindinafune zilizonse Zachijeremani, ngakhale chinenero nkhondoyo itatha. Chotero tsopano ndinangogamulapo kudzilanga mwa kuphunziranso Chijeremani. Komabe, zimene ndinati ndi chilangozo zinasanduka dalitso. Lekani ndifotokoze.
Ndinapeza ponse paŵiri mabuku ena Achijeremani ndi Achitcheki ndi kuyamba kudziphunzitsa kutembenuza Chijeremani m’Chitcheki ndi Chitcheki m’Chijeremani. Ntchito imeneyi sinangokhala yothandiza kwambiri pa zimene zikanakhala zotulukapo zoipa za kubindikiridwa pandekha komanso inatumikira chifuno china chabwino pambuyo pake.
Kumasuka ndi Kupitiriza Kulalikira
Potsiriza, patapita miyezi isanu ndi itatu ndili m’ndende pandekha, mlandu wanga unazengedwa. Anandipeza ndi mlandu wofuna kugwetsa boma nandipatsa chilango cha zaka ziŵiri m’ndende. Popeza kuti ndinali nditakhalamo kale miyezi 15 ndipo chilengezo cha kukhululukira akaidi chinali chitaperekedwa pamene pulezidenti watsopano anasankhidwa, ndinamasulidwa.
Ndili m’ndende ndinapemphera kuti banja lathu lisade nkhaŵa za ine, ndipo nditabwerera kunyumba, ndinapeza kuti pemphero limeneli linali litayankhidwa. Atate anali dokotala, ndipo analimbikitsa odwala awo ambiri kuphunzira Baibulo. Chotero, Amayi anali kuchititsa maphunziro pafupifupi 15 mlungu ndi mlungu! Ndiponso, Atate anali kuchititsa phunziro la magazini a Nsanja ya Olonda m’kagulu kena. Analinso kutembenuza mabuku ena a Watch Tower Society kuchotsa m’Chijeremani kuika m’Chitcheki, ndipo mlongo wanga ankatayipa makope ake. Choncho ndinadziloŵetsa panthaŵi yomweyo m’ntchito yauzimu ndipo posapita nthaŵi ndinali kuchititsa maphunziro a Baibulo.
Ntchito Yatsopano
Tsiku lina masana pamene mvula inali kugwa mu November 1954, munthu wina analiza belu pakhomo. Yemwe anaima pakhomopo anali Konstantin Paukert, mmodzi wa awo amene anali kutsogolera pa ntchito yolalikira, madzi akumatsereremba pa lenikhothi yake yapulasitiki yotumbuluka modera. Kaŵirikaŵiri, ankakonda kulankhula ndi Atate kapena ndi mlongo wanga Pavel, koma panthaŵiyi anandipempha kuti: “Kodi sintingapite kokayenda kwa kanthaŵi?”
Tinayenda kwa kanthaŵi osalankhulana, oyenda m’khwalala angapo akumadutsa. Kuunika koziya kwa magetsi a m’khwalala kunaonekera pang’ono pamadzi omwe anali pathala yakudayo. Konstantin anayang’ana kumbuyo; m’khwalala munalibe munthu aliyense. “Kodi ungakonde kutithandiza pa ntchito ina?” anafunsa mwadzidzidzi. Ngakhale kuti ndinazizwa, ndinavomera mwa kungogwedeza mutu. “Tifuna kuchita ntchito yotembenuza,” iye anapitiriza. “Uyenera kupeza malo kogwirira ntchito koma osati kunyumba ndipo osati ndi munthu wodziŵika kwa apolisi.”
Patapita masiku angapo, ndinali mu ofesi m’kanyumba kena ka okwatirana okalamba amene sindinawadziŵe nkomwe. Iwo anali odwala a Atate, ndipo anali atangoyamba kuphunzira nawo Baibulo. Motero, kuphunzira kwanga Chijeremani m’ndende kunakhala kothandiza, pakuti panthaŵiyo tinkatembenuza mabuku athu kuchotsa m’Chijeremani kuika m’Chitcheki.
Patapita milungu ingapo, abale Achikristu otsogolera pa ntchitoyo anaponyedwa m’ndende, ndi Mbale Paukert yemwe. Komabe, ulaliki wathu sunaimitsidwe. Akazi, kuphatikizapo ine ndi Amayi, tinathandizira kusamalira timagulu tophunzira Baibulo ndi utumiki wathu Wachikristu. Mlongo wanga Pavel, ngakhale kuti anali wachichepere, anali wamtengatenga wa mabuku ndi malangizo a gulu m’mbali yonse ya dzikoli kumene amalankhula Chitcheki.
Bwenzi Lokondedwa
Chakumapeto kwa 1957, Jaroslav Hála, Mboni imene inaponyedwa m’ndende mu 1952 ndi kupatsidwa chilango cha zaka 15, anamasulidwa kwa kanthaŵi kuti akalandire mankhwala. Mwamsanga Pavel anakaonana naye, ndipo posapita nthaŵi Jaroslav anatanganitsidwanso ndi kuthandiza abale. Pokhala wodziŵa bwino zinenerozo, anayamba kuchita yochuluka ya ntchito yotembenuza.
Tsiku lina madzulo chapakati pa 1958, Jaroslav anatipempha ine ndi Pavel kupita kukawongola miyendo. Kaŵirikaŵiri zimenezi zinkachitika pokambitsirana nkhani za gulu, popeza kuti m’chipinda chathu a boma anaikamo kachipangizo kojambula mawu. Koma atalankhula ndi Pavel pambali, anampempha kuyembekeza pa benchi m’paki pamene aŵirife tinapitiriza kuyenda. Titakambitsirana pang’ono za ntchito yanga, iye anandifunsa ngati, mosasamala kanthu za thanzi lake losakhala bwino ndi mtsogolo mwake mosatsimikizirika, ndingakwatiwe naye.
Ndinadabwa nako kufunsira koona mtima ndi kolunjika kwa munthu amene ndinamlemekeza kwambiri, ndipo ndinavomera mosataya nthaŵi. Ndinakondana kwambiri ndi amayi ake a Jaroslav chifukwa cha kutomerana kwathu. Iwo anali Mkristu wodzozedwa. Iwo ndi amuna awo anali pakati pa Mboni zoyamba m’Prague chakumapeto kwa ma 1920. Aŵiriwo anaponyedwa m’ndende ndi Anazi m’nkhondo yadziko yachiŵiri, ndipo amuna awo anafera m’ndende Yachikomyunizimu mu 1954.
Tisanakwatirane, Jára, monga mmene tinkamtchera, anamuitana akuluakulu a boma. Anamuuza kuti asankhepo pa kuchitidwa opaleshoni chifukwa cha chibayo chake chosatha—kumene panthaŵiyo kukanatanthauza kuvomera kuthiridwa mwazi—kapena kutsiriza ukaidi wake wonse. Popeza kuti anakana opaleshoni, ndiye kuti anali ndi zaka zina pafupifupi khumi zokhala m’ndende. Ndinasankha kumuyembekezera.
Nthaŵi ya Kuyesedwa ndi ya Kulimba Mtima
Kuchiyambi kwa 1959, Jára anatengedwa kupita kundende, ndipo posapita nthaŵi, tinalandira kalata yosonyeza kuti anali kukondwa. Ndiyeno panapita nthaŵi yaitali kuti tilandire kalata ina imene inatithetsa nzeru. Imeneyo inasonyeza kugwiritsidwa mwala, chisoni, ndi nkhaŵa, ngati kuti Jára anachita tondovi. “Kalatayi iyenera kuti inalembedwa ndi munthu wina,” amake anatero. Koma dzanja linali lake!
Aŵirife, ine ndi amake, tinamlembera ndi kumtchulira za kudalira kwathu Mulungu ndi kumlimbikitsa. Patapita milungu yambiri, kalata ina inafika, yothetsa nzeru kwambiri. “Sindiye amene analemba imeneyi,” anateronso amake. Komatu, dzanja linalidi lake, ndipo inali ndi mawu ake amene anakonda. Sitinalandirenso makalata ena, ndipo sitinaloledwe kukamuona.
Nayenso Jára analandira makalata ozunguza mutu amene anawayesa kuti anachokera kwa ife. M’makalatawo, amake anamuimba mlandu chifukwa chowasiya okha mu ukalamba wawo, ndipo ine ndinamuuza kuti ndinakwiya chifukwa chakuti ndinamuyembekezera nthaŵi yaitali yonseyo. Awanso anafanana ndendende ndi manja athu ndi makambidwe athu. Poyamba nayenso anazunguzika mutu, koma pambuyo pake sanakhulupirire kuti ndife amene tinalemba makalatawo.
Tsiku lina munthu wina anatulukira pakhomo pathu, nandipatsa kaphukusi, napita msangamsanga. Mkati mwake munali masamba ambiri a mapepala a fodya amene analembedwapo timawu tating’ono kwambiri. Jára anali atajambula makalata amene anawayesa kuti ndife tinalemba, limodzinso ndi makalata ake ambiri osapendedwa ndi boma. Titalandira makalata ameneŵa amene anazembetsedwa ndi mkaidi amene sanali Mboni yemwe anamasulidwa, mitima yathu inakhazikika pansi chotani nanga ndipo tinathokoza Yehova! Mpaka lero sitidziŵa mmene kuyesayesa kwauchiŵanda kwa kuswa umphumphu wathu kumeneku kunayambira ndi yemwe anakuyambitsa.
Pambuyo pake, amake Jára analoledwa kukaona mwana wawo. Panthaŵi zimenezi, ndinkatsagana nawo kufika pachipata cha ndende ndi kuona mmene kamkazi kokalamba ndi kochepa thupi kameneka kanasonyezera kulimba mtima kwambiri. Alonda akupenya, iwo ankagwirana chanza ndi mwana wawo ndi kumpatsa kabuku kojambula kakang’ono kwambiri. Ngakhale kuti kuwaona akuchita zimenezo kukanatanthauza chilango chowopsa, makamaka kwa mwana wawo, iwo anadalira Yehova, pozindikira kuti kusamalira thanzi lauzimu ndiko kofunika choyamba nthaŵi zonse.
Pambuyo pake, mu 1960, boma linalengeza kuti lakhululukira onse, ndipo Mboni zochuluka zinamasulidwa m’ndende. Jára anabwera kunyumba, ndipo m’milungu ingapo, tinakhala banja lachimwemwe lokwatirana chatsopano.
Kusintha Moyo Wanga
Jára anapatsidwa ntchito yoyendayenda, akumatumikira abale m’dziko lonseli. Mu 1961 anauzidwa kulinganiza kalasi loyamba la Sukulu Yautumiki Waufumu kudera limene amalankhula Chitcheki m’dzikoli, limodzinso ndi kusaemalira makalasi ena ambiri a sukuluyo pambuyo pake.
Chifukwa cha kusintha m’zandale mu Czechoslovakia mu 1968, chaka chotsatira ambiri a ife tinakhoza kufika pa Msonkhano wa Mitundu Yonse wa Mboni za Yehova wa “Mtendere pa Dziko Lapansi” ku Nuremberg, Germany. Komabe, akuluakulu a boma sanalole Jára kutuluka m’dziko. Ife ena tinatenga zithunzithunzi zamasilaidi za msonkhano waukulu umenewo, ndipo Jára anali ndi mwaŵi wa kusonyeza programu yolimbitsa chikhulupiriro ya zithunzithunzi zimenezo m’dziko lonseli. Ambiri anafuna kuonerera programuyo mobwerezabwereza.
Sitinadziŵe kuti imeneyi inali nthaŵi yomaliza imene Jára anali kuchezetsa abale. Kuchiyambi kwa 1970, iye anadwala kwambiri. Nthenda yake yosatha, imene anapirira nayo, inayambukira imso zake, ndipo kulephera kwa imso zake kugwira ntchito kunamupha. Anafa ali ndi zaka 48.
Ndilimbika Mothandizidwa ndi Yehova
Ndinafedwa munthu amene ndinamkonda kwambiri. Koma thandizo lamwamsanga linaperekedwa m’gulu la Mulungu, pakuti ndinaloledwa kutembenuza mabuku a Baibulo. Mofanana ndi liŵiro lopatsirana kamtengo, ndinalingalira kuti mwamuna wanga anandipatsira kamtengo kuti ndipitirize ntchito yotsala imene anali kuchita.
Ambirife ku Eastern Europe tinatumikira Yehova kwa zaka zoposa 40 pansi pa chiletso cha Komyunizimu. Ndiyeno mu 1989, chifukwa cha kuchotsedwa kwa Iron Curtain, moyo kunoko unayamba kusintha kwambiri. Pamene kuli kwakuti ndinkalakalaka kuti Mboni za Yehova zidzachitire msonkhano mu Strahov Stadium bwalo lamaseŵera lalikulu kwambirilo mu Prague, sindinakhulupirire kuti zolakalaka zimenezi zikachitika. Komabe, mu August 1991, zinachitikadi mwanjira yodabwitsa pamene oposa 74,000 anasonkhana pa kulambira kwachimwemwe!
Czechoslovakia anasiya kukhalako mu January 1993 pamene dzikolo linagaŵidwa m’maiko aŵiri—Czech Republic ndi Slovakia. Tinakondwera chotani nanga pamene, pa September 1, 1993, Czech Republic inavomereza Mboni za Yehova mwalamulo!
Malinga ndi zimene ndakumana nazo m’moyo, ndikudziŵa kuti Yehova nthaŵi zonse amatisungira dalitso, malinga ngati timlola kutiphunzitsa kuŵerenga masiku athu. (Salmo 90:12) Nthaŵi zonse ndimapemphera kwa Mulungu kuti andiphunzitse kuŵerenga masiku anga otsala m’dongosolo ili la zinthu kuti m’masiku osaŵerengeka amene ali mtsogolo m’dziko lake latsopano, ndikakhale pakati pa atumiki ake achimwemwe.
[Chithunzi patsamba 20]
Amayi ndi atate
[Chithunzi patsamba 22]
Msonkhano m’nkhalango mu 1949 pansi pa chiletso: 1. Mlongo wanga Pavel, 2. Amayi, 3. Atate, 4. Ineyo, 5. Mbale Hála
[Chithunzi patsamba 23]
Ndi mwamuna wanga, Jára
[Chithunzi patsamba 24]
Amayi ake a Jára ndi buku lojambula limene iwo anampatsa mozembetsa
[Chithunzi patsamba 25]
Lerolino ndikugwira ntchito panthambi m’Prague